Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
31 : 7

۞ يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ خُذُواْ زِينَتَكُمۡ عِندَ كُلِّ مَسۡجِدٖ وَكُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ وَلَا تُسۡرِفُوٓاْۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ

E inu ana a Adam! Tengani (valani) zovala zanu zabwino pamene mukukapemphera Swala iliyonse ndipo idyani ndi kumwa; koma musapyoze muyeso. Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso (oononga). info
التفاسير:

external-link copy
32 : 7

قُلۡ مَنۡ حَرَّمَ زِينَةَ ٱللَّهِ ٱلَّتِيٓ أَخۡرَجَ لِعِبَادِهِۦ وَٱلطَّيِّبَٰتِ مِنَ ٱلرِّزۡقِۚ قُلۡ هِيَ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا خَالِصَةٗ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ

Nena: “Ndani waletsa zokongoletsa za Allah (zovala), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo Ake ndi zakudya zabwino?” Nena: “Zinthu zimenezo nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wa pa dziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M’menemo ndi momwe tikulongosolera Ayah (Zathu) kwa anthu ozindikira.”[181] info

[181] Padali anthu ena omwe adali ndi chikhulupiliro choti kuvala nsanza ndi kudya zinthu zosakoma ndiko kumuopa Allah. Mpaka masiku ano alipobe anthu oganiza motere. Ndipo nchifukwa chake Allah akuvumbulutsa Ayah izi kuti kutero sindiko kumuopa Allah.

التفاسير:

external-link copy
33 : 7

قُلۡ إِنَّمَا حَرَّمَ رَبِّيَ ٱلۡفَوَٰحِشَ مَا ظَهَرَ مِنۡهَا وَمَا بَطَنَ وَٱلۡإِثۡمَ وَٱلۡبَغۡيَ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَأَن تُشۡرِكُواْ بِٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ سُلۡطَٰنٗا وَأَن تَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Nena (kwa iwo): “Ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu zauve zoonekera ndi zobisika, ndi machimo, ndi kuwukira (atsogoleri) popanda choonadi, ndi kumphatikiza Allah ndi chomwe sadachitsitsire umboni (wakuti chiphatikizidwe ndi Iye); ndiponso (waletsa) kumunenera Allah zimene simukuzidziwa.”[182] info

[182] Choipa nchoipa basi. Kaya kuchichita moonekera kapena mobisa, nchoipabe.

التفاسير:

external-link copy
34 : 7

وَلِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٞۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ لَا يَسۡتَأۡخِرُونَ سَاعَةٗ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ

M’badwo ulionse uli ndi nthawi yakeyake (yofera). Ndipo nthawi yawo ikadza sangaichedwetse ngakhale ola limodzi, ndiponso sangaifulumizitse. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 7

يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ إِمَّا يَأۡتِيَنَّكُمۡ رُسُلٞ مِّنكُمۡ يَقُصُّونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِي فَمَنِ ٱتَّقَىٰ وَأَصۡلَحَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

E inu ana a Adam! Akakudzerani Atumiki ochokera mwa inu namakuuzani zivumbulutso Zanga, (avomereni), choncho omwe adzitchinjiriza ku zoletsedwa ndi kuchita zabwino, sipadzakhala mantha pa iwo ndiponso sadzadandaula. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 7

وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱسۡتَكۡبَرُواْ عَنۡهَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu nadzitukumula nazo, awo ndi anthu a ku Moto, adzakhala mmenemo nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 7

فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ أُوْلَٰٓئِكَ يَنَالُهُمۡ نَصِيبُهُم مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُنَا يَتَوَفَّوۡنَهُمۡ قَالُوٓاْ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ قَالُواْ ضَلُّواْ عَنَّا وَشَهِدُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَنَّهُمۡ كَانُواْ كَٰفِرِينَ

Kodi ndani woipitsitsa koposa munthu wopekera bodza Allah kapena wotsutsa zivumbulutso Zake? Iwo gawo (lachakudya chimene) adawalembera liwafika (pano pa dziko lapansi ngakhale kuti ngosakhulupirira mwa Allah). Kufikira pomwe adzawadzera atumiki Athu (angelo kudzatenga miyoyo yawo), nawapatsadi imfa uku akunena: “Kodi zili kuti zija munkazipembedza kusiya Allah?” Adzati: “Zatisowa.” Ndipo adzadzichitira okha umboni kuti iwo adali okana (Allah). info
التفاسير: