(Adzakhala) akuyenda mothamanga mitu ili m’mwamba ndipo maso awo osatha kuphethira, ndipo m’mitima mwawo muli mopanda kanthu (mopanda ganizo lililonse chifukwa cha kudzadzidwa ndi mantha).
Choncho usaganize kuti Allah Ngwakuswa lonjezo Lake kwa atumiki Ake. Ndithu Allah ndi mwini mphamvu (salephera chilichonse), Ngobwezera chilango mwaukali.
Izi zikukwana kukhala phunziro kwa anthu kuti achenjezedwe nazo, ndi kuti azindikire kuti Iye (Allah) ndi Mulungu Mmodzi basi, ndikuti eni nzeru akumbukire.