Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
43 : 14

مُهۡطِعِينَ مُقۡنِعِي رُءُوسِهِمۡ لَا يَرۡتَدُّ إِلَيۡهِمۡ طَرۡفُهُمۡۖ وَأَفۡـِٔدَتُهُمۡ هَوَآءٞ

(Adzakhala) akuyenda mothamanga mitu ili m’mwamba ndipo maso awo osatha kuphethira, ndipo m’mitima mwawo muli mopanda kanthu (mopanda ganizo lililonse chifukwa cha kudzadzidwa ndi mantha). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 14

وَأَنذِرِ ٱلنَّاسَ يَوۡمَ يَأۡتِيهِمُ ٱلۡعَذَابُ فَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ رَبَّنَآ أَخِّرۡنَآ إِلَىٰٓ أَجَلٖ قَرِيبٖ نُّجِبۡ دَعۡوَتَكَ وَنَتَّبِعِ ٱلرُّسُلَۗ أَوَلَمۡ تَكُونُوٓاْ أَقۡسَمۡتُم مِّن قَبۡلُ مَا لَكُم مِّن زَوَالٖ

Ndipo achenjeze anthu za tsiku lomwe chilango chidzawadzera; ndipo amene ankadzichitira okha zoipa adzakhala akunena: “Mbuye wathu! Tichedwetseni kanthawi kochepa (tipatseninso mwawi kuti tibwelere pa dziko); tikayankhe kuitana Kwanu ndi kuwatsata atumiki.” (Adzauzidwa): “Kodi simunkalumbira kale kuti inu simudzachoka (pa dziko)?” info
التفاسير:

external-link copy
45 : 14

وَسَكَنتُمۡ فِي مَسَٰكِنِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَتَبَيَّنَ لَكُمۡ كَيۡفَ فَعَلۡنَا بِهِمۡ وَضَرَبۡنَا لَكُمُ ٱلۡأَمۡثَالَ

“Chikhalirecho mudakhala m’malo mommuja mwa omwe adadzichitira okha zoipa; ndipo kudaonekeratu poyera kwa inu mmene tidawachitira (powaononga); ndipo tidakufotokozerani mafanizo (osiyanasiyana koma inu mudatsutsa).” info
التفاسير:

external-link copy
46 : 14

وَقَدۡ مَكَرُواْ مَكۡرَهُمۡ وَعِندَ ٱللَّهِ مَكۡرُهُمۡ وَإِن كَانَ مَكۡرُهُمۡ لِتَزُولَ مِنۡهُ ٱلۡجِبَالُ

Ndithudi, adachita ziwembu zawo, koma ziwembu zawo zili kwa Allah (akuzidziwa bwinobwino); ndipo ziwembu zawozo angakhale zitatha kuchotsetsa mapiri (sangamchite kanthu Mtumiki Muhammad (s.a.w} popeza Allah wamteteza). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 14

فَلَا تَحۡسَبَنَّ ٱللَّهَ مُخۡلِفَ وَعۡدِهِۦ رُسُلَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٞ ذُو ٱنتِقَامٖ

Choncho usaganize kuti Allah Ngwakuswa lonjezo Lake kwa atumiki Ake. Ndithu Allah ndi mwini mphamvu (salephera chilichonse), Ngobwezera chilango mwaukali. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 14

يَوۡمَ تُبَدَّلُ ٱلۡأَرۡضُ غَيۡرَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱلسَّمَٰوَٰتُۖ وَبَرَزُواْ لِلَّهِ ٱلۡوَٰحِدِ ٱلۡقَهَّارِ

(Likumbukireni) tsiku lomwe nthaka iyi idzasinthidwa kukhala nthaka ina (yachilendo), ndi thambonso (lidzakhala lina), ndipo iwo (anthu onse adzatuluka m’manda mwawo) adzaonekera pamaso pa Allah Mmodzi Wamphamvu (zopanda malire). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 14

وَتَرَى ٱلۡمُجۡرِمِينَ يَوۡمَئِذٖ مُّقَرَّنِينَ فِي ٱلۡأَصۡفَادِ

Ndipo oipa udzawaona tsiku limenelo atanjatidwa ndi unyolo. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 14

سَرَابِيلُهُم مِّن قَطِرَانٖ وَتَغۡشَىٰ وُجُوهَهُمُ ٱلنَّارُ

Zovala zawo zidzakhala zaphula, ndipo Moto udzavindikira nkhope zawo; info
التفاسير:

external-link copy
51 : 14

لِيَجۡزِيَ ٱللَّهُ كُلَّ نَفۡسٖ مَّا كَسَبَتۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ

Kuti Allah aulipire mzimu uliwonse pa zomwe udakolola; ndithu; Allah Ngwachangu pakuwerengera. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 14

هَٰذَا بَلَٰغٞ لِّلنَّاسِ وَلِيُنذَرُواْ بِهِۦ وَلِيَعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَا هُوَ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ وَلِيَذَّكَّرَ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Izi zikukwana kukhala phunziro kwa anthu kuti achenjezedwe nazo, ndi kuti azindikire kuti Iye (Allah) ndi Mulungu Mmodzi basi, ndikuti eni nzeru akumbukire. info
التفاسير: