Ndipo (akumbutse anthu ako) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu pamene adakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe adakuzunzani ndi chilango choipa. Ankazinga (kupha) ana anu aamuna ndi kuwasiya amoyo ana anu aakazi; ndithu m’zimenezi mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.”
Ndipo Mûsa adati (kwa anthu ake): “Ngati inu mukana (pakusiya kuthokoza) pamodzi ndi onse a m’dziko, (Allah salabadira chilichonse pa zimenezo), ndithudi Allah Ngwachikwanekwane; Ngotamandidwa.”