“Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”
“Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”
[223] Chilangocho chidali chimphepo choononga chomwe chinagumula nyumba ndi kulowa m’mphuno za adani a Allah ndi kutulukira kokhalira kwawo. Chinkangowagwetsa chafufumimba kotero kuti anthu adali lambilambi ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza.
Ndipo adatsatizidwa ndi tembelero pa moyo wapano padziko lapansi ndi tsiku la Qiyâma (tsiku la chiweruziro). Dziwani! Ndithu Âdi adakana Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka Âdi, anthu a Hûd!.