ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا

external-link copy
61 : 11

۞ وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ هُوَ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱسۡتَعۡمَرَكُمۡ فِيهَا فَٱسۡتَغۡفِرُوهُ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي قَرِيبٞ مُّجِيبٞ

Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).” info
التفاسير: