“Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”
“Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”
“Ndipo kulangiza kwanga sikungakuthandizeni ngati ntafuna kukulangizani, ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera. Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa.”
Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”