[460] Tanena kale mndemanga 7 yamu surat - Dhuha kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) asadapatsidwe uneneri wake ndi Allah adali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi Mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira ya chiongoko. Choncho tsiku lina pamene adali ku phanga la Hiraa, pafupi ndi Makka ali mkati mopemphera, Mngelo adamuonekera mwadzidzidzi nati: “Iwe Muhammad! Ine ndine Jiburil (Gabrie!) ndipo iwe ndiwe Mtumiki wa Allah kwa zolengedwa zonse!” Pambuyo pake adamuuza kuti: “werenga!” Mneneri adayankha: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Jiburil uja adamgwira ndi kumpana mwamphamvu mpaka adavutika kwambiri. Adamsiyanso ndi kumuuza: “werenga!” Mneneri adayankha monga adamuyankhira poyamba mpaka kadakwana katatu akumuchita zokhazokhazo. Kenaka adamuwerengera ma Ayah kuchokera 1 mpaka 5. Ma Ayah amenewa ndiwo oyamba kuvumbulutsidwa m’Qur’an.
[462] Ayah 3 ndi 5 Mtumiki (s.a.w) akuyankhidwa pa kunena kwake kwa kuti: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Choncho Allah akumuuza kuti Iye ndi Mfulu weniweni, ndi Yemwe adawaphunzitsa anthu kulemba ndi cholembera ndi zonse zomwe sadali kuzidziwa. Kwa ufulu Wake wochuluka ndi mphamvu Zake pa chilichonse, sichovuta kwa Iye (Allah) kumphunzitsa Mtumiki Wake kuwerenga molakatula.
[463] Tanthauzo lake nkuti musanyengedwe ndi chumacho chifukwa chakuti, popanda chikaiko, mubwerera kwa Mbuye wanu ndipo chumacho sichidzakuthandizani chilichonse pa maso Pake.