Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
56 : 7

وَلَا تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بَعۡدَ إِصۡلَٰحِهَا وَٱدۡعُوهُ خَوۡفٗا وَطَمَعًاۚ إِنَّ رَحۡمَتَ ٱللَّهِ قَرِيبٞ مِّنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo musaononge pa dziko pambuyo popakonza. Mpempheni (Allah) mwamantha ndi mwakhumbo. Ndithu chifundo cha Allah chili pafupi kwa (anthu Ake ) ochita zabwino.[184] info

[184] Chifundo cha Allah chimawafika anthu omwe amachitiranso chifundo anzawo. Ndipo amene sachitira anzawo chifundo sangapezenso chifundo cha Allah. Choncho tiyeni tilimbikire kuthandiza ofooka ndi osowa chithandizo. Ngati sititero ndiye kuti chifundo cha Allah chidzakhala kutali nafe.

التفاسير: