Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Al-Munâfiqûn

external-link copy
1 : 63

إِذَا جَآءَكَ ٱلۡمُنَٰفِقُونَ قَالُواْ نَشۡهَدُ إِنَّكَ لَرَسُولُ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ إِنَّكَ لَرَسُولُهُۥ وَٱللَّهُ يَشۡهَدُ إِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ لَكَٰذِبُونَ

Akakudzera achiphamaso akunena kuti: “Tikuikira umboni kuti ndithu iwe ndiwe Mtumiki wa Allah, ndipo Allah akudziwa kuti iwe ndiwe mtumiki Wake. Ndipo Allah akuikira umboni kuti achiphamaso ngabodza (pa zomwe akunena). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 63

ٱتَّخَذُوٓاْ أَيۡمَٰنَهُمۡ جُنَّةٗ فَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِنَّهُمۡ سَآءَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Kulumbira kwawo (kwa bodza) akuchita kukhala chotetezera (chuma chawo ndi matupi awo). Tero atsekereza (anthu kuyenda) panjira ya Allah. Ndithu nzoipa zedi zimene amachita. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 63

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ ءَامَنُواْ ثُمَّ كَفَرُواْ فَطُبِعَ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَهُمۡ لَا يَفۡقَهُونَ

Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakhulupirira (modzionetsera), kenako adakana (mobisa). Choncho mitima yawo idatsekedwa kotero kuti iwo sangathe kuzindikira (chimene chingawapulumutse ku chilango cha Allah.) info
التفاسير:

external-link copy
4 : 63

۞ وَإِذَا رَأَيۡتَهُمۡ تُعۡجِبُكَ أَجۡسَامُهُمۡۖ وَإِن يَقُولُواْ تَسۡمَعۡ لِقَوۡلِهِمۡۖ كَأَنَّهُمۡ خُشُبٞ مُّسَنَّدَةٞۖ يَحۡسَبُونَ كُلَّ صَيۡحَةٍ عَلَيۡهِمۡۚ هُمُ ٱلۡعَدُوُّ فَٱحۡذَرۡهُمۡۚ قَٰتَلَهُمُ ٱللَّهُۖ أَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ

Ndipo ukawaona, akukondweretsa matupi awo; ndipo akayankhula umvetsera zoyankhula zawo (chifukwa chakuthwa kwa malirime awo, pomwe mkati mwawo ndiming’oma yopanda kanthu); iwo ali ngati matsinde a mitengo yomwe yayadzamiritsidwa (ku chipupa); (mwa iwo mulibe moyo). Mkuwe uliwonse (umene akuumva) akuganiza kuti ukulinga iwo, (chifukwa cha kuzindikira chinyengo chawo); iwowa ndiadani; chenjerani nawo. Allah awatembelere! Mwanjira yanji akuchotsedwa (ku choonadi)! info
التفاسير: