Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
99 : 6

وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ نَبَاتَ كُلِّ شَيۡءٖ فَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهُ خَضِرٗا نُّخۡرِجُ مِنۡهُ حَبّٗا مُّتَرَاكِبٗا وَمِنَ ٱلنَّخۡلِ مِن طَلۡعِهَا قِنۡوَانٞ دَانِيَةٞ وَجَنَّٰتٖ مِّنۡ أَعۡنَابٖ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُشۡتَبِهٗا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٍۗ ٱنظُرُوٓاْ إِلَىٰ ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَيَنۡعِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكُمۡ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ

Iye ndi Yemwe amavumbwitsa mvula kuchokera kumwamba. Ndi madzi a mvulayo timameretsa mmera wa chinthu chilichonse. Ndipo m’menemo tikuphukitsa masamba obiriwira, tikutulutsa mmenemo njere zosanjikana; ndiponso m’kanjedza m’mikoko mwake mumatuluka maphava ogoweka (ndizipatso). Ndipo amakumeretserani minda ya mphesa, mzitona ndi makomamanga, ofanana ndi osafanana. Tapenyani zipatso zake pamene zikupatsa ndi kupsa kwake. Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira. info
التفاسير: