Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
80 : 6

وَحَآجَّهُۥ قَوۡمُهُۥۚ قَالَ أَتُحَٰٓجُّوٓنِّي فِي ٱللَّهِ وَقَدۡ هَدَىٰنِۚ وَلَآ أَخَافُ مَا تُشۡرِكُونَ بِهِۦٓ إِلَّآ أَن يَشَآءَ رَبِّي شَيۡـٔٗاۚ وَسِعَ رَبِّي كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًاۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ

Ndipo anthu ake adakangana naye (pomuuza kuti: “Bwanji ukusiya chipembedzo chamakolo ako; uona malaulo”). (Iye) adati: “Kodi Mukukangana nane pa za Allah pomwe Iye wanditsogolera? Ndipo Sindingaope zimene mukumphatikiza Naye, kupatula Mbuye wanga akafuna chinthu, (apo chiyenera kuchitika). Mbuye wanga akudziwa chinthu chilichonse bwinobwino. Bwanji simulalikika?” info
التفاسير: