Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
160 : 6

مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ عَشۡرُ أَمۡثَالِهَاۖ وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَا وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho. Ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho (popanda kuonjezera). Ndipo iwo sadzaponderezedwa.[176] info

[176] China mwa chifundo cha Allah pa zolengedwa zake ndiko kuti adzamulipira munthu pa tsiku la chimaliziro mosiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa. Ngati adachita chabwino chimodzi, adzamulipira mphoto ya zinthu khumi zoposera pa chabwino chimodzicho ndipo ngati adachita choipa, sadzamuonjezera malipiro a choipacho koma adzamulipira chofanana ndi choipacho. Tanthauzo lake nkuti chabwino chimodzi malipiro ake ndi zabwino khumi; pomwe choipa chimodzi mphoto yake ndi choipanso chimodzi.

التفاسير: