Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
45 : 5

وَكَتَبۡنَا عَلَيۡهِمۡ فِيهَآ أَنَّ ٱلنَّفۡسَ بِٱلنَّفۡسِ وَٱلۡعَيۡنَ بِٱلۡعَيۡنِ وَٱلۡأَنفَ بِٱلۡأَنفِ وَٱلۡأُذُنَ بِٱلۡأُذُنِ وَٱلسِّنَّ بِٱلسِّنِّ وَٱلۡجُرُوحَ قِصَاصٞۚ فَمَن تَصَدَّقَ بِهِۦ فَهُوَ كَفَّارَةٞ لَّهُۥۚ وَمَن لَّمۡ يَحۡكُم بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Ndipo m’menemo (m’buku la Taurat) tidawalamula kuti: “Munthu aphedwe chifukwa chopha mnzake, ndi kuti diso kwa diso, mphuno kwa mphuno; khutu kwa khutu; dzino kwa dzino, ndiponso kubwezerana mabala.” Koma amene wakhululuka ndiye kuti dipo likhala kwa iye. Ndipo amene saweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa iwowo ndiwo anthu ochita zoipa. info
التفاسير: