Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
34 : 43

وَلِبُيُوتِهِمۡ أَبۡوَٰبٗا وَسُرُرًا عَلَيۡهَا يَتَّكِـُٔونَ

Ndipo nyumba zawo kukhala ndi zitseko ndi makama (mabedi) omwe amayadzamira (zonsezo kukhala za Siliva). info
التفاسير:

external-link copy
35 : 43

وَزُخۡرُفٗاۚ وَإِن كُلُّ ذَٰلِكَ لَمَّا مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُتَّقِينَ

Ndiponso ndi zokongoletsa za golide. Koma zonsezo sikanthu ayi, ndi chisangalalo chabe cha dziko lapansi (chosakhalira kutha); ndipo tsiku lachimaliziro lomwe lili kwa Mbuye wako ndi la oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 43

وَمَن يَعۡشُ عَن ذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ نُقَيِّضۡ لَهُۥ شَيۡطَٰنٗا فَهُوَ لَهُۥ قَرِينٞ

Ndipo amene akunyozera kukumbukira (Allah) Wachifundo chambiri, timpatsa satana, kuti iye akhale bwenzi lake (lotsagana nalo). info
التفاسير:

external-link copy
37 : 43

وَإِنَّهُمۡ لَيَصُدُّونَهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ

Ndipo iwo amawatsekereza ku njira zabwino ndi kumaganiza kuti iwo ngoongoka. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 43

حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَنَا قَالَ يَٰلَيۡتَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَ بُعۡدَ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرِينُ

Kufikira pamene adzatidzera (tsiku la Qiyâma, uku akulowetsedwa ku Moto). Adzati (kumuuza satana): “Kalanga ine! Pakati pa ine ndi iwe pakadakhala ntunda wa pakati pa kuvuma ndi kuzambwe (kutalikirana kwathu).” Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi! info
التفاسير:

external-link copy
39 : 43

وَلَن يَنفَعَكُمُ ٱلۡيَوۡمَ إِذ ظَّلَمۡتُمۡ أَنَّكُمۡ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ

(Allah adzawauza kuti): “Ndipo lero sikukuthandizani kukhala limodzi kwanu m’chilango pakuti mudadzichitira nokha zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 43

أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ أَوۡ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَمَن كَانَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

Kodi ungathe kuwamveretsa agonthi, kapena ungathe kuwaongola akhungu ndi amene ali mkusokera koonekera? info
التفاسير:

external-link copy
41 : 43

فَإِمَّا نَذۡهَبَنَّ بِكَ فَإِنَّا مِنۡهُم مُّنتَقِمُونَ

Ngati titakuchotsa (padziko usadaone chilango chawo, usakhale ndi chikaiko), ndithu Ife tiwalanga iwo. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 43

أَوۡ نُرِيَنَّكَ ٱلَّذِي وَعَدۡنَٰهُمۡ فَإِنَّا عَلَيۡهِم مُّقۡتَدِرُونَ

Kapena tikusonyeza zimene tidawalonjeza (uona ndi maso ako usadafe). Ndithu Ife tili ndi mphamvu pa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 43

فَٱسۡتَمۡسِكۡ بِٱلَّذِيٓ أُوحِيَ إِلَيۡكَۖ إِنَّكَ عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

Choncho, gwiritsa zimene zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu iwe uli pa njira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 43

وَإِنَّهُۥ لَذِكۡرٞ لَّكَ وَلِقَوۡمِكَۖ وَسَوۡفَ تُسۡـَٔلُونَ

Ndithu iyi (Qur’an) ndi ulemelero wako ndi anthu ako; ndipo posachedwa mufunsidwa (za ulemelero umenewu). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 43

وَسۡـَٔلۡ مَنۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رُّسُلِنَآ أَجَعَلۡنَا مِن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ءَالِهَةٗ يُعۡبَدُونَ

Ndipo afunse atumiki Athu amene tidawatumiza iwe usadadze: “Kodi tidapanga milungu ina kuti ipembedzedwe, osati (Allah) Wachifundo chambiri?” info
التفاسير:

external-link copy
46 : 43

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَقَالَ إِنِّي رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndithu tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa Zathu kwa Farawo ndi nduna zake; ndipo adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mbuye wa zolengedwa.” info
التفاسير:

external-link copy
47 : 43

فَلَمَّا جَآءَهُم بِـَٔايَٰتِنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَضۡحَكُونَ

Koma pamene adawadzera ndi zisonyezo zathu, basi iwo adali kuziseka. info
التفاسير: