Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
11 : 41

ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰٓ إِلَى ٱلسَّمَآءِ وَهِيَ دُخَانٞ فَقَالَ لَهَا وَلِلۡأَرۡضِ ٱئۡتِيَا طَوۡعًا أَوۡ كَرۡهٗا قَالَتَآ أَتَيۡنَا طَآئِعِينَ

Kenako adalunjika ku thambo (malunjikidwe ogwirizana ndimomwe Iye alili mosafanana ndi zolengedwa zake), pomwe ilo (thambolo) lidali utsi. Ndipo adati kwa ilo ndi nthaka: “Idzani, mofuna kapena mokakamizidwa (tsatirani lamulo Langa).” Izo zidayankha kuti: “Tadza mofuna.” info
التفاسير: