Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
40 : 34

وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعٗا ثُمَّ يَقُولُ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ أَهَٰٓؤُلَآءِ إِيَّاكُمۡ كَانُواْ يَعۡبُدُونَ

Ndipo (kumbuka iwe Mneneri) tsiku limene (Allah) adzawasonkhanitsa onse ndi kunena kwa angelo: “Kodi awa amapembedza inu?” info
التفاسير:

external-link copy
41 : 34

قَالُواْ سُبۡحَٰنَكَ أَنتَ وَلِيُّنَا مِن دُونِهِمۖ بَلۡ كَانُواْ يَعۡبُدُونَ ٱلۡجِنَّۖ أَكۡثَرُهُم بِهِم مُّؤۡمِنُونَ

Adzanena: “Kuyera konse Nkwanu (simungakhale limodzi ndi milungu ina!) Inu ndinu Mtetezi wathu, osati iwo. Koma amagwadira majini (ziwanda); ambiri mwa iwo (anthu) adakhulupirira izo (ziwanda).” info
التفاسير:

external-link copy
42 : 34

فَٱلۡيَوۡمَ لَا يَمۡلِكُ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٖ نَّفۡعٗا وَلَا ضَرّٗا وَنَقُولُ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلنَّارِ ٱلَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ

(Allah adzawauza iwo:) “Lero aliyense mwa inu sangathe kudzetsa zabwino ngakhale masautso pa ena.” Ndipo tidzawauza amene adadzichitira okha zoipa: “Lawani chilango cha Moto chimene munkachitsutsa.” info
التفاسير:

external-link copy
43 : 34

وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ قَالُواْ مَا هَٰذَآ إِلَّا رَجُلٞ يُرِيدُ أَن يَصُدَّكُمۡ عَمَّا كَانَ يَعۡبُدُ ءَابَآؤُكُمۡ وَقَالُواْ مَا هَٰذَآ إِلَّآ إِفۡكٞ مُّفۡتَرٗىۚ وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٞ

Ndipo Ayah Zathu zofotokoza momveka zikamawerengedwa kwa iwo, amanena, “Sichina uyu (Muhammad {s.a.w}) koma ndi munthu yemwe akufuna kukutsekerezani mapemphero amene amapemphera makolo anu.” Ndipo akunena: “Sichina iyi (Qur’an) koma ndibodza lopekedwa.” Ndipo amene sadakhulupirire akunena pa choona pamene chawadzera: “Sikanthu ichi, koma ndi matsenga woonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
44 : 34

وَمَآ ءَاتَيۡنَٰهُم مِّن كُتُبٖ يَدۡرُسُونَهَاۖ وَمَآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمۡ قَبۡلَكَ مِن نَّذِيرٖ

Ndipo (ngakhale awa Arabu) sitidawapatse mabuku oti aziwawerenga (buku ili lisanadze); ndipo sitidawatumizirenso mchenjezi patsogolo pako. (Nanga akudziwa bwanji kuti Qur’an iyi ndiyonama?) info
التفاسير:

external-link copy
45 : 34

وَكَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ وَمَا بَلَغُواْ مِعۡشَارَ مَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ فَكَذَّبُواْ رُسُلِيۖ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ

Ndipo amene adalipo iwowo kulibe, adatsutsa, ndipo (awa Arabu) sadapeze gawo limodzi m’magawo khumi a zomwe tidawapatsa iwowo, koma adatsutsa atumiki Anga (pa zomwe adawabweretsera). Nanga chidali bwanji chilango Changa (pa iwo)? info
التفاسير:

external-link copy
46 : 34

۞ قُلۡ إِنَّمَآ أَعِظُكُم بِوَٰحِدَةٍۖ أَن تَقُومُواْ لِلَّهِ مَثۡنَىٰ وَفُرَٰدَىٰ ثُمَّ تَتَفَكَّرُواْۚ مَا بِصَاحِبِكُم مِّن جِنَّةٍۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا نَذِيرٞ لَّكُم بَيۡنَ يَدَيۡ عَذَابٖ شَدِيدٖ

Nena: “Ndithu ndikukulangizani chinthu chimodzi, kuti muimilire chifukwa cha Allah; awiriawiri ndi mmodzimmodzi, ndipo kenako mulingalire; (muona kuti uyu Muhammad {s.a.w} chilichonse chomwe akunena nchoona. Ndiponso muona kuti) mnzanuyu alibe misala. Iye, sichina, koma ndimchenjezi wanu chisanadze chilango chaukali.” info
التفاسير:

external-link copy
47 : 34

قُلۡ مَا سَأَلۡتُكُم مِّنۡ أَجۡرٖ فَهُوَ لَكُمۡۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٞ

Nena: “Chilichonse ndakupemphani kukhala malipiro (othandizira kufikitsa uthenga kwa anthu) ndichanu, malipiro anga ali kwa Allah basi. Ndipo Iye ndi Mboni pachilichonse.” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 34

قُلۡ إِنَّ رَبِّي يَقۡذِفُ بِٱلۡحَقِّ عَلَّٰمُ ٱلۡغُيُوبِ

Nena: “Ndithu Mbuye wanga amaponya choonadi (ponseponse kotero kuti chonama chimathawa). Ngodziwa zedi (zinthu) zobisika.” info
التفاسير: