[301] Alipo ena pakati pa anthu amene amangonena ndi malirime awo okha kuti: “Takhulupilira Allah.” Koma mmodzi wawo akavutitsidwa chifukwa cha chikhulupiliro chakecho, amatuluka m’chipembedzomo. Ndipo masautso a anthu amati ndicho chifukwa chomwe chidawachotsetsa m’chipembedzocho. Komatu chilango cha Allah nchosafanana ndi chilango cha anthu. Chofunika kwa iwo nkupilira ndi kulimba mtima; osatekeseka ndi chilichonse ngakhale choononga moyo wawo.