Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
14 : 28

وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُۥ وَٱسۡتَوَىٰٓ ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمٗا وَعِلۡمٗاۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo (Mûsa) pamene adakula nsinkhu wake ndi kulingana bwino tidampatsa nzeru ndi maphunziro. Ndipo umo ndimomwe timawalipirira ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 28

وَدَخَلَ ٱلۡمَدِينَةَ عَلَىٰ حِينِ غَفۡلَةٖ مِّنۡ أَهۡلِهَا فَوَجَدَ فِيهَا رَجُلَيۡنِ يَقۡتَتِلَانِ هَٰذَا مِن شِيعَتِهِۦ وَهَٰذَا مِنۡ عَدُوِّهِۦۖ فَٱسۡتَغَٰثَهُ ٱلَّذِي مِن شِيعَتِهِۦ عَلَى ٱلَّذِي مِنۡ عَدُوِّهِۦ فَوَكَزَهُۥ مُوسَىٰ فَقَضَىٰ عَلَيۡهِۖ قَالَ هَٰذَا مِنۡ عَمَلِ ٱلشَّيۡطَٰنِۖ إِنَّهُۥ عَدُوّٞ مُّضِلّٞ مُّبِينٞ

Ndipo (tsiku lina) adalowa mu mzinda mozemba, eni m’zindawo osadziwa. Ndipo adapeza m’menemo anthu awiri akumenyana, mmodzi wochokera ku gulu lake, ndipo winayo wochokera kwa adani ake. Tsono wa kugulu lake uja adampempha chithandizo pa mdani wake uja, ndipo Mûsa adammenya chibagera mpaka kumupha (mdaniyo). Adanena: “Iyi (ndachitayi) ndintchito ya satana; ndithu iye ndimdani wosokeretsa, woonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 28

قَالَ رَبِّ إِنِّي ظَلَمۡتُ نَفۡسِي فَٱغۡفِرۡ لِي فَغَفَرَ لَهُۥٓۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ndadzichitira zoipa ndekha! Choncho ndikhululukireni!” Tero (Allah) adamkhululukira (chifukwa sadalinge kupha). Ndithu Iye (Allah) Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 28

قَالَ رَبِّ بِمَآ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ فَلَنۡ أَكُونَ ظَهِيرٗا لِّلۡمُجۡرِمِينَ

Adati: “E Mbuye wanga! Chifukwa cha kuti mwandidalitsa, sindidzakhala mthangati wa oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
18 : 28

فَأَصۡبَحَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ خَآئِفٗا يَتَرَقَّبُ فَإِذَا ٱلَّذِي ٱسۡتَنصَرَهُۥ بِٱلۡأَمۡسِ يَسۡتَصۡرِخُهُۥۚ قَالَ لَهُۥ مُوسَىٰٓ إِنَّكَ لَغَوِيّٞ مُّبِينٞ

Choncho kudamuchera mu mzindamo (m’mawa mwake) uku ali wodzazidwa ndi mantha akuyembekezera (kuti chiyani chimpeze pa zimene zidachitika); pompo munthu uja adampempha dzulo chithandizo ankamuitana (kuti amthandize kumenyana ndi m’dani wake wina). Mûsa adamuuza: “Ndithudi ndiwe wopotoka owonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 28

فَلَمَّآ أَنۡ أَرَادَ أَن يَبۡطِشَ بِٱلَّذِي هُوَ عَدُوّٞ لَّهُمَا قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ أَتُرِيدُ أَن تَقۡتُلَنِي كَمَا قَتَلۡتَ نَفۡسَۢا بِٱلۡأَمۡسِۖ إِن تُرِيدُ إِلَّآ أَن تَكُونَ جَبَّارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا تُرِيدُ أَن تَكُونَ مِنَ ٱلۡمُصۡلِحِينَ

Choncho pamene adafuna kumpanda, yemwe ndi mdani wa awiriwo, (uja wofuna chithandizo kwa Mûsa adaganiza kuti Mûsa afuna kuti ampande iye), ndipo adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukufuna kundipha monga momwe udaphera munthu uja dzulo? Iwe sufuna china koma kukhala wodzitukumula (wankhanza) pa dziko, ndipo sukufuna kukhala mmodzi mwa ochita zabwino (oyanjanitsa okangana ndi kukonza zinthu).” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 28

وَجَآءَ رَجُلٞ مِّنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّ ٱلۡمَلَأَ يَأۡتَمِرُونَ بِكَ لِيَقۡتُلُوكَ فَٱخۡرُجۡ إِنِّي لَكَ مِنَ ٱلنَّٰصِحِينَ

(Farawo zitamfika mphekesera kuti Mûsa wapha munthu pothangata mu Israyeli, adalamula kuti Mûsa paliponse pomwe angapezeke, agwidwe ndi kuphedwa). Choncho munthu adadza akuthamanga kuchokera kumalekezero a m’zindawo. Adati: “E iwe Mûsa! Akuluakulu akukuchitira upo kuti akuphe choncho choka (m’dziko muno). Ndithu ine ndine mmodzi mwa okufunira iwe zabwino.” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 28

فَخَرَجَ مِنۡهَا خَآئِفٗا يَتَرَقَّبُۖ قَالَ رَبِّ نَجِّنِي مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo adachoka mu mzindawo ali woopa uku akuyembekezera (kumpeza choipa kuchokera kwa adani ake). Adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu ochita zoipa.” info
التفاسير: