Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
58 : 21

فَجَعَلَهُمۡ جُذَٰذًا إِلَّا كَبِيرٗا لَّهُمۡ لَعَلَّهُمۡ إِلَيۡهِ يَرۡجِعُونَ

Choncho adawaphwanya (mafanowo) zidutswazidutswa kupatula lalikulu lawo (sadaliswe) kuti iwo alibwelere (ndi kulifunsa zimene zachitika). info
التفاسير:

external-link copy
59 : 21

قَالُواْ مَن فَعَلَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَآ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ

(Iwo parnene adafika kumafano awo) adati: “Ndani wachita ichi pa milungu yathu? Ndithu iye ndi m’modzi wa ochita zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
60 : 21

قَالُواْ سَمِعۡنَا فَتٗى يَذۡكُرُهُمۡ يُقَالُ لَهُۥٓ إِبۡرَٰهِيمُ

Adati: “Tidamumva m’nyamata wina akuitchula (moipa); amatchedwa Ibrahim.” info
التفاسير:

external-link copy
61 : 21

قَالُواْ فَأۡتُواْ بِهِۦ عَلَىٰٓ أَعۡيُنِ ٱلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَشۡهَدُونَ

Adati: “Mubweretseni pamaso pa anthu kuti amuone.” info
التفاسير:

external-link copy
62 : 21

قَالُوٓاْ ءَأَنتَ فَعَلۡتَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَا يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ

Adati: “Kodi ndiwedi wachita ichi ku milungu yathu, E, iwe Ibrahim?” info
التفاسير:

external-link copy
63 : 21

قَالَ بَلۡ فَعَلَهُۥ كَبِيرُهُمۡ هَٰذَا فَسۡـَٔلُوهُمۡ إِن كَانُواْ يَنطِقُونَ

(Iye) adati: “(Iyayi), koma wachita ichi ndi mkulu wawoyu. Choncho afunseni (kuti akuuzeni zenizeni) ngati amatha kuyankhula.” info
التفاسير:

external-link copy
64 : 21

فَرَجَعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ فَقَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ أَنتُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Ndipo adadzitembenukira okha ndikunena kuti: “Ndithu inu ndinu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
65 : 21

ثُمَّ نُكِسُواْ عَلَىٰ رُءُوسِهِمۡ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَا هَٰٓؤُلَآءِ يَنطِقُونَ

Kenako adazyolitsa mitu yawo (ndikubwerera kuumbuli wawo) nanena kuti: “Ndithu iwe ukudziwa kuti izi siziyankhula (nchifukwa ninji ukutichita chipongwe)?” info
التفاسير:

external-link copy
66 : 21

قَالَ أَفَتَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا يَضُرُّكُمۡ

(Iye) adati: “Kodi mukupembedza zomwe sizingakuthandizeni chilichonse, kusiya Allah, zomwenso sizingakupatseni masautso?” info
التفاسير:

external-link copy
67 : 21

أُفّٖ لَّكُمۡ وَلِمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

“Kuyaluka nkwanu ndi zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah. Kodi simuganizira?” info
التفاسير:

external-link copy
68 : 21

قَالُواْ حَرِّقُوهُ وَٱنصُرُوٓاْ ءَالِهَتَكُمۡ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ

(Iwo) adati: “Mtentheni; ndipo pulumutsani milungu yanu, ngati inu mungathe kuchita zimenezi.” info
التفاسير:

external-link copy
69 : 21

قُلۡنَا يَٰنَارُ كُونِي بَرۡدٗا وَسَلَٰمًا عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ

Tidati: “E iwe Moto! Khala kuzizira ndiponso mtendere kwa Ibrahim.” info
التفاسير:

external-link copy
70 : 21

وَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدٗا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَخۡسَرِينَ

Ndipo adamfunira chiwembu; koma tidawachita kukhala otaika zedi. info
التفاسير:

external-link copy
71 : 21

وَنَجَّيۡنَٰهُ وَلُوطًا إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَا لِلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo tidampulumutsa iye ndi Luti kupita ku dziko lomwe tidalidalitsa ku zolengedwa. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 21

وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ نَافِلَةٗۖ وَكُلّٗا جَعَلۡنَا صَٰلِحِينَ

Ndipo (Ibrahim) tidampatsa Ishaq ndi kuonjezera Ya’qub, ndipo tidawachita onse kukhala abwino. info
التفاسير: