Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
60 : 17

وَإِذۡ قُلۡنَا لَكَ إِنَّ رَبَّكَ أَحَاطَ بِٱلنَّاسِۚ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلرُّءۡيَا ٱلَّتِيٓ أَرَيۡنَٰكَ إِلَّا فِتۡنَةٗ لِّلنَّاسِ وَٱلشَّجَرَةَ ٱلۡمَلۡعُونَةَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِۚ وَنُخَوِّفُهُمۡ فَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا طُغۡيَٰنٗا كَبِيرٗا

Ndipo (kumbuka) pamene tidakuuza kuti ndithu Mbuye wako wawazungulira anthu (mowadziwa bwinobwino;) ndipo sitidawachite maloto omwe tidakuonetsa koma kuti akhale mayeso kwa anthu, (kuti kodi akhulupirira kapena sakhulupirira), ndiponso (kutchula kwa) rntengo wotembeleredwa m’Qur’an (ndimayetseronso kwa iwo;) ndipo tikuwachenjeza, koma (machenjezo athu) sakuwaonjezera china koma kulumpha malire kwakukulu basi. info
التفاسير: