[214] Allah akuti: Sikunayenere kwa anthu kudabwa ndi kutsutsa chivumbulutso chathu kwa munthu wochokera mwa iwo yemwe cholinga chake nkuti achenjeze anthu za chilango cha Allah ndi kuti awauze nkhani zabwino amene mwa iwo akhulupilira. Ndiponso nkosayenera kwa iwo kumunenera Muhammadi (s.a.w), Mtumiki wathu, kuti iye ndi wa matsenga.
[215] Mbuye wanu ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka. Ndipo dzuwa adalipanga kuti lizipereka kuwala ku zolengedwa; naonso mwezi kuti uzitumiza kuunika. Ndipo mwezi adaupangira njira momwe umayenda. Ndipo kuunika kwake kumakhala kosiyanasiyana chifukwa cha masitesheniwa. Izi nkuti zikuthangateni powerengera nthawi, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka. Allah adalenga zimenezi ncholinga chanzeru zakuya.