[323] Ndime iyi ikunenetsa kuti sikoyenera kwa Msilamu kutsata maganizo ake pa chinthu chimene Allah ndi Mtumiki walamulapo lamulo, koma afunika kutsatira lamulo la Allah ndi Mtumiki, ndipo asakhale ndi chifuniro pa zinthu zomwe nza chipembedzo koma agonjere zimene Allah walamula ndi Mtumiki Wake. Kunyoza lamulo la Allah ndi Mtumiki kumachititsa kuti munthu atayike.
[324] Polamula chinthu kuti chichitike kapena chisachitike, pafunika kuti iwe wolamula ukhale woyamba kutsata malamulowo. Ngati sutero, ndiye kuti malamulo akowo sangakhale ndi mphamvu. Mu ndime iyi muli chilolezo chomukwatira mkazi yemwe wasiyidwa ukwati ndi mwana yemwe adangoleredwa chabe ndi munthu amene amatcha mwanayo kuti ndi mwana wake chifukwa chomulera. Kalelo zoterezi sizimaloledwa. Choncho Mtumiki (s.a.w) adauzidwa kuti achite iye mwini zimenezi pofuna kuthetsa chikhalidwecho.
[325] Ndime iyi ikumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti palibe vuto pa iye ngakhale tchimo kapena kudzudzulidwa pa chomwe Allah wamulamula kuchichita monga kukwatira akazi ambiri. Ayuda amamunyoza ndi kumudzudzula chifukwa chokwatira akazi ambiri. Koma Allah adawayankha ndi mawu ake oti: “Iyi ndi njira ya Allah yomwe idalipo pa Aneneri akale! Daud adakwatira akazi 100. Ndipo Sulaimani akazi 300.
[326] Ndime iyi ikumuuza Mtumiki kuti amene adamulamula kuti awatsanzire pa zimene ankachita ndi iwo amene ankafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu, ndipo samaopa kudzudzulidwa ndi aliyense pa chomwe Allah wawalamula kuchita, koma ankangoopa Allah Yekha. Choncho nawenso tsanzira khalidwe lawo ndi kuopa Allah Yekha.
[327] (“Khaatamu Nabiyyina) “Mneneri wotsirizira” tanthauzo lake ndi kuti Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndimneneri womalizira; palibe mneneri wina pambuyo pake mpaka kutha kwadziko lapansi. Ayah imeneyi ikutsutsa zonena za Akadiyani ndi enanso omwe akumutcha mtsogoleri wawo kuti ndi mneneri.