قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

Al-Ahzâb

external-link copy
1 : 33

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ ٱتَّقِ ٱللَّهَ وَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقِينَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمٗا

E iwe Mneneri! Muope Allah, ndipo usamvere osakhulupirira ndi achiphamaso. Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri; Wanzeru zakuya (m’zoyankhula ndi m’zochita Zake).[316] info

[316] Sura iyi ikutchedwa Sura ya Ahzab kutanthauza kuti namtindi wa anthu. Zimenezi zidali chonchi kuti pamene Chisilamu chimafala mu mzinda wa Madina momwe mumakhalanso Ayuda, adachita nsanje yaikulu Ayudawo. Ndipo akuluakulu awo adaganiza zopita ku Makka kukakopa Arabu akumeneko kuti athandizane kuthira nkhondo Asilamu. Choncho Arabu a ku Makka adauza mitundu yonse yopembedza mafano kuti akamthire nkhondo Muhammad (s.a.w) ndi kuthetseratu chipembedzo cha Chisilamu. Tero adagwirizana ndipo adauzinga mzinda wa Madina mbali zonse. Koma Allah adatumiza angelo ndi chimphepo chamkuntho chomwe chidamwazamwaza katundu wawo. Pachifukwa ichi, onse adathawa.

التفاسير:

external-link copy
2 : 33

وَٱتَّبِعۡ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٗا

Ndipo tsata zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako (pozigwiritsa ntchito). Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 33

وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلٗا

Ndipo yadzamira kwa Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Msungi ndi Mtetezi (wako). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 33

مَّا جَعَلَ ٱللَّهُ لِرَجُلٖ مِّن قَلۡبَيۡنِ فِي جَوۡفِهِۦۚ وَمَا جَعَلَ أَزۡوَٰجَكُمُ ٱلَّٰٓـِٔي تُظَٰهِرُونَ مِنۡهُنَّ أُمَّهَٰتِكُمۡۚ وَمَا جَعَلَ أَدۡعِيَآءَكُمۡ أَبۡنَآءَكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ قَوۡلُكُم بِأَفۡوَٰهِكُمۡۖ وَٱللَّهُ يَقُولُ ٱلۡحَقَّ وَهُوَ يَهۡدِي ٱلسَّبِيلَ

Allah sadaike m’chifuwa cha munthu mitima iwiri. Ndipo sadachite akazi anu amene mukuwayesa ena mwa iwo monga amayi anu, kukhala mayi anu enieni. Ndipo sadachite ana anu ongowalera kukhala ana anu enieni (monga inu mukuwatchulira). Zimenezo ndi zolankhula zanu za pakamwa panu chabe. Koma Allah akunena choona; Iye akuongolera ku njira yoongoka. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 33

ٱدۡعُوهُمۡ لِأٓبَآئِهِمۡ هُوَ أَقۡسَطُ عِندَ ٱللَّهِۚ فَإِن لَّمۡ تَعۡلَمُوٓاْ ءَابَآءَهُمۡ فَإِخۡوَٰنُكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَمَوَٰلِيكُمۡۚ وَلَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٞ فِيمَآ أَخۡطَأۡتُم بِهِۦ وَلَٰكِن مَّا تَعَمَّدَتۡ قُلُوبُكُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورٗا رَّحِيمًا

Aitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndichilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, (aitaneni ngati) ndiabale anu pachipembedzo; ndiponso ndi anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pa zimene mitima yanu yachita mwadala. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 33

ٱلنَّبِيُّ أَوۡلَىٰ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ مِنۡ أَنفُسِهِمۡۖ وَأَزۡوَٰجُهُۥٓ أُمَّهَٰتُهُمۡۗ وَأُوْلُواْ ٱلۡأَرۡحَامِ بَعۡضُهُمۡ أَوۡلَىٰ بِبَعۡضٖ فِي كِتَٰبِ ٱللَّهِ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُهَٰجِرِينَ إِلَّآ أَن تَفۡعَلُوٓاْ إِلَىٰٓ أَوۡلِيَآئِكُم مَّعۡرُوفٗاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورٗا

Mneneri ngofunika kwambiri kwa okhulupirira kuposa moyo wawo, (matupi awo ndi chuma chawo); ndipo akazi ake ndi amayi awo (amayi a Asilamu; nkoletsedwa kuwakwatira pambuyo pa imfa yake). Ndipo achibale pakati pawo ngoyenera (kulandira zamasiye pamalamulo a) m’buku la Allah kuposa Asilamu ena ngakhalenso Amuhajirina (amene adasamuka ku Makka kupita ku Madina chifukwa cha chipembedzo cha Chisilamu). Kupatula ngati mutachita zabwino kwa anzanu (sikolakwika). Izi zidalembedwa kale m’buku.[317] info

[317] Ayah iyi ikufotokoza zakuletsedwa kukwatira akazi a Mtumiki (s.a.w), mwini wake atamwalira chifukwa choti akazi a Mtumiki (s.a.w) ndiamayi a Asilamu onse.

التفاسير: