قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

صفحہ نمبر:close

external-link copy
25 : 2

وَبَشِّرِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ كُلَّمَا رُزِقُواْ مِنۡهَا مِن ثَمَرَةٖ رِّزۡقٗا قَالُواْ هَٰذَا ٱلَّذِي رُزِقۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَأُتُواْ بِهِۦ مُتَشَٰبِهٗاۖ وَلَهُمۡ فِيهَآ أَزۡوَٰجٞ مُّطَهَّرَةٞۖ وَهُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake (ndi patsogolo pake). Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: “Izi ndizomwe tidapatsidwa kale,” (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m’maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. Koma makomedwe ake ngosiyana). Ndiponso akalandira m’menemo akazi oyeretsedwa (kuuve wamtundu uliwonse); ndipo iwo adzakhala m’menemo nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 2

۞ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَسۡتَحۡيِۦٓ أَن يَضۡرِبَ مَثَلٗا مَّا بَعُوضَةٗ فَمَا فَوۡقَهَاۚ فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فَيَعۡلَمُونَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡۖ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَيَقُولُونَ مَاذَآ أَرَادَ ٱللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلٗاۘ يُضِلُّ بِهِۦ كَثِيرٗا وَيَهۡدِي بِهِۦ كَثِيرٗاۚ وَمَا يُضِلُّ بِهِۦٓ إِلَّا ٱلۡفَٰسِقِينَ

Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 2

ٱلَّذِينَ يَنقُضُونَ عَهۡدَ ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مِيثَٰقِهِۦ وَيَقۡطَعُونَ مَآ أَمَرَ ٱللَّهُ بِهِۦٓ أَن يُوصَلَ وَيُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 2

كَيۡفَ تَكۡفُرُونَ بِٱللَّهِ وَكُنتُمۡ أَمۡوَٰتٗا فَأَحۡيَٰكُمۡۖ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يُحۡيِيكُمۡ ثُمَّ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Kodi mungamkane chotani Allah chikhalirecho inu mudali akufa ndipo adakupatsani moyo (nakuikani pa dziko lapansi)? Kenako adzakupatsani imfa (ikakwana nthawi yanu yofera). Kenako adzakuukitsani (ndikukutulutsani m’manda). Ndipo kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mudali kuchita). info
التفاسير:

external-link copy
29 : 2

هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ لَكُم مَّا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰٓ إِلَى ٱلسَّمَآءِ فَسَوَّىٰهُنَّ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖۚ وَهُوَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ

Iye ndi Yemwe adakulengerani zonse za m’dziko lapansi, kenako adalunjika ku thambo nakonza thambo zisanu ndi ziwiri. Iye Ngodziwa chinthu chilichonse.[2] info

[2] Adalunjika ku thambo molingana ndi mmene Allah yo alili osati mofanana ndi zolengedwa Zake.

التفاسير: