[8] Hajj ndi Umrah ndimapemphero amene sangachitike pamalo pena paliponse kupatula mu mzinda wa Makka. Kachitidwe ka mapemphero awiriwa nkofanana. Koma pamakhala kusiyana pang’ono pakati pa Hajj ndi Umrah. Kusiyana kwake kuli motere: Hajj siichitika nthawi iliyonse koma m’miyezi yake yodziwika. Ndipo kutha kwamiyezi ya Hajj ndi masiku khumi am’khumi loyamba a m’mwezi wa Thul Hijjah. Pomwe Umrah ikhoza kuchitika m’mwezi uliwonse umene munthu wafuna.
Pamapiripo Chisilamu chisanadze adaikapo mafano omwe anthu achikunja panthawiyo adali kuwapembedza. Tero pamene Chisilamu chidadza Asilamu ena sadali kuona bwino kukachitira mapemphero pa mapiriwo poganizira za mafano amene adalipo kalelo. Koma adawauza kuti palibe kuipa kulikonse kuchitirapo mapemphero pa malopo chifukwa mafanowo adawachotsapo.
[9] Nkofunika kwa munthu aliyense amene wachidziwa choona kuchita izi:-
a) Kuchivomereza choonacho.
b) Kuchitsata.
c) Kuchifalitsa.
d) Kuchiphunzitsa.
Choncho, masheikh ndi maulama ali ndi mwawi pokhala ndi ntchito yapamwambayi. Achite ntchitoyi modzipereka kwatunthu, mwaulere kapena molandira malipiro ngati alipo. Apitirize kuigwira ntchitoyi pamoyo wawo wonse ngakhale atakumana ndi zovuta pa ntchitoyi. Ntchitoyi njomwe aneneri a Allah adali kugwira. Tero aigwire motsanzira momwe aneneri a Allah adali kuigwilira ntchitoyi pamakhalidwe awo ndi machitidwe awo onse. Kubisa komwe kwanenedwa m’ndimeyi sikubisa mawu a Allah kokha, komanso kubisa maphunziro a zam’dziko ofunika kwa anthu.
Chisilamu chikulimbikitsa kuti ngati munthu akudziwa chilichonse chomwe chili ndi phindu kwa anthu awaphunzitse anzake, asawabisire chifukwa choopa kuti nzeruyo angaitulukire anthu ambiri ndi kuti iye sadzapatsidwa ulemu kapena kuopa kuti ena angampose. Maganizo otere ngosafunika m’Chisilamu.
[10] Tanthauzo la ndime iyi ndikuti Mulungu wanu wompembedza ndi mmodzi.
Palibe wompembedza mwachoonadi pa dziko lonse lapansi ndi kumwamba koma Iye Yekha. Iye Ngwachifundo chambiri, Wachisoni kwa zolengedwa Zake; Woyera ndiponso Wotukuka pachikhalidwe Chake chonse. Ndipo ali kutali ndi zimene akumunenerazo. Kodi asatukuke chotani ku zimene akumunenerazo chikhalirecho Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi zonse zam’menemo monga nyenyezi zikuluzikulu zomwe zikuyenda m’menemo mwadongosolo Lake lakuya popanda kuwombana ina ndi inzake. Ndipo m’dziko lapansi adaikamo zolengedwa zambiri zododometsa zomwe zikusonyeza mphamvu Zake zoposa, monga nyama zamoyo ndizomera zosiyanasiyana. Ndipo zikulozera kuti alipo amene adazilenga ndi amene akuziyang’anira yemwe ndi Allah. Dongosolo la zinthuzi likusonyeza kuti Allah ndi mmodzi chifukwa chakuti pakadakhala anzake othandizana naye pakadakhala chisokonezo, wina akadafuna china pomwe wina akufuna china.