قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
96 : 5

أُحِلَّ لَكُمۡ صَيۡدُ ٱلۡبَحۡرِ وَطَعَامُهُۥ مَتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِلسَّيَّارَةِۖ وَحُرِّمَ عَلَيۡكُمۡ صَيۡدُ ٱلۡبَرِّ مَا دُمۡتُمۡ حُرُمٗاۗ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِيٓ إِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ

Nkololezedwa kwa inu kusaka nyama za m’nyanja ndi chakudya chake (chomwe chapezeka m’nyanjamo chitafa chokha). Chimenecho ndi kamba wanu (inu amene simuli pa ulendo) ndiponso a pa ulendo. Kwaletsedwa kwa inu kusaka za pamtunda pomwe muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Opani Allah Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 5

۞ جَعَلَ ٱللَّهُ ٱلۡكَعۡبَةَ ٱلۡبَيۡتَ ٱلۡحَرَامَ قِيَٰمٗا لِّلنَّاسِ وَٱلشَّهۡرَ ٱلۡحَرَامَ وَٱلۡهَدۡيَ وَٱلۡقَلَٰٓئِدَۚ ذَٰلِكَ لِتَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَأَنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٌ

Allah wapanga Ka’aba kukhala nyumba yopatulika, ndikukhala pamalo popezera zosowa za anthu. Ndipo adapanganso miyezi (inayi) yopatulika, ndi kupereka nyama zansembe ku Makka zovekedwa makoza monga zisonyezo (kusonyeza kuti zikupita ku Makka). Zonsezi nkuti mudziwe kuti Allah akudziwa za kumwamba ndi pansi, ndikuti Allah Ngodziwa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
98 : 5

ٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ وَأَنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Dziwani kuti ndithudi, Allah Ngolanga mwaukali. Ndikutinso Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
99 : 5

مَّا عَلَى ٱلرَّسُولِ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تُبۡدُونَ وَمَا تَكۡتُمُونَ

Pa mtumiki palibe china koma kufikitsa chabe (uthenga). Ndipo Allah akudziwa zimene mukuzionetsera poyera ndi zimene mukuzibisa. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 5

قُل لَّا يَسۡتَوِي ٱلۡخَبِيثُ وَٱلطَّيِّبُ وَلَوۡ أَعۡجَبَكَ كَثۡرَةُ ٱلۡخَبِيثِۚ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

Nena (kwa aliyense kuti): “Zoipa ndi zabwino sizingafanane ngakhale kutakusangalatsa kuchuluka kwa zoipazo; choncho opani Allah, E! Inu eni nzeru kuti mupambane.” info
التفاسير:

external-link copy
101 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَسۡـَٔلُواْ عَنۡ أَشۡيَآءَ إِن تُبۡدَ لَكُمۡ تَسُؤۡكُمۡ وَإِن تَسۡـَٔلُواْ عَنۡهَا حِينَ يُنَزَّلُ ٱلۡقُرۡءَانُ تُبۡدَ لَكُمۡ عَفَا ٱللَّهُ عَنۡهَاۗ وَٱللَّهُ غَفُورٌ حَلِيمٞ

E inu amene mwakhulupirira! Musamafunse za zinthu zomwe zitasonyezedwa kwa inu zikuipirani. Ndipo ngati muzifunsa pomwe Qur’an ikuvumbulutsidwa, zionetsedwa kwa inu. Allah wakhululuka zimenezo. Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza. info
التفاسير:

external-link copy
102 : 5

قَدۡ سَأَلَهَا قَوۡمٞ مِّن قَبۡلِكُمۡ ثُمَّ أَصۡبَحُواْ بِهَا كَٰفِرِينَ

Anthu amene adalipo kale inu musanadze, adazifunsapo zotere. Ndipo pachifukwa chimenecho adasanduka osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
103 : 5

مَا جَعَلَ ٱللَّهُ مِنۢ بَحِيرَةٖ وَلَا سَآئِبَةٖ وَلَا وَصِيلَةٖ وَلَا حَامٖ وَلَٰكِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَۖ وَأَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ

Allah sadaike (kuletsedwa kwamtundu uliwonse) pa nyama yotchedwa Bahira[166], ngakhale Saiba[167], ngakhale Wasila[168], ngakhalenso Hami[169]. Koma amene sadakhulupirire akumpekera Allah bodza. Ndipo ambiri a iwo sagwiritsa ntchito nzeru zawo. info

[166] Bahira: Ngamila yaikazi yomwe umasungidwa mkaka wake kusungira mafano, ndipo palibe amaloledwa kuikama mkaka.
[167] Saiba: Ngamila yaikazi yomwe idali kusiyidwa kuti izidya yokha, komanso imaletsedwa kunyamulirapo katundu, chifukwa idali yolemekedzera mafano.
[168] Wasila: Ngamila yaikazi yomwe imasiyidwa kuwasiyira mafano chifukwa choti yabereka kamwana kakakazi pa bele lake loyamba ndi lachiwiri.
[169] Hami: Ngamila yaimuna yomwe imasiyidwa kuwasiyira mafano chifukwa chakuti yamaliza ntchito yopereka mabele ku ngamila zazikazi zingapo.

التفاسير: