قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
51 : 5

۞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ ٱلۡيَهُودَ وَٱلنَّصَٰرَىٰٓ أَوۡلِيَآءَۘ بَعۡضُهُمۡ أَوۡلِيَآءُ بَعۡضٖۚ وَمَن يَتَوَلَّهُم مِّنكُمۡ فَإِنَّهُۥ مِنۡهُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Ayuda ndi Akhrisitu musawapale ubwenzi (nkumawauza chinsinsi chanu). Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi atetezi kwa wina ndi mnzake. Amene awapale ubwenzi mwa inu, ndiye kuti iye ndi m’modzi wa iwo. Ndithudi, Allah satsogolera anthu ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 5

فَتَرَى ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ يُسَٰرِعُونَ فِيهِمۡ يَقُولُونَ نَخۡشَىٰٓ أَن تُصِيبَنَا دَآئِرَةٞۚ فَعَسَى ٱللَّهُ أَن يَأۡتِيَ بِٱلۡفَتۡحِ أَوۡ أَمۡرٖ مِّنۡ عِندِهِۦ فَيُصۡبِحُواْ عَلَىٰ مَآ أَسَرُّواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ نَٰدِمِينَ

Uwaona omwe m’mitima mwawo muli matenda (a chinyengo) akuthamangira kwa iwo (Ayuda) uku akuti: “Tikuopa lingatigwere tsoka (ngati Asilamuwa atagwa m’tsoka), koma posachedwapa Allah abweretsa lamulo logonjetsa (midzi), kapena chinthu china chochokera kwa Iye (monga kuwaulula achinyengo zomwe akubisa m’mitima mwawo). Choncho adzasanduka odzinena chifukwa cha zomwe adabisa m’mitima mwawo. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 5

وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَهَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ أَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ إِنَّهُمۡ لَمَعَكُمۡۚ حَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡ فَأَصۡبَحُواْ خَٰسِرِينَ

Ndipo amene adakhulupirira nayamba kunena (chitaululika chinyengo cha achinyengowo): “Kodi awa si omwe adali kulumbilira dzina la Allah m’kulumbilira kwawo kwamphamvu kuti iwo ali pamodzi ndi inu?” Zochita zawo zaonongeka. Tero akhala otaika. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَن يَرۡتَدَّ مِنكُمۡ عَن دِينِهِۦ فَسَوۡفَ يَأۡتِي ٱللَّهُ بِقَوۡمٖ يُحِبُّهُمۡ وَيُحِبُّونَهُۥٓ أَذِلَّةٍ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ أَعِزَّةٍ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ يُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلَا يَخَافُونَ لَوۡمَةَ لَآئِمٖۚ ذَٰلِكَ فَضۡلُ ٱللَّهِ يُؤۡتِيهِ مَن يَشَآءُۚ وَٱللَّهُ وَٰسِعٌ عَلِيمٌ

E inu amene mwakhulupirira! Amene mwa inu asiye chipembedzo chake, ndiye kuti posachedwapa Allah abweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda; odzichepetsa kwa okhulupirira (anzawo); amphamvu kwa osakhulupirira; omenyera nkhondo chipembedzo cha Allah, saopa kudzudzula kwa odzudzula. Umenewu ndi ubwino wa Allah; amaupereka kwa amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mataya; Ngodziwa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 5

إِنَّمَا وَلِيُّكُمُ ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُمۡ رَٰكِعُونَ

Ndithu mtetezi wanu ndi Allah ndi Mtumiki wake ndi omwe akhulupirira omwe akupemphera Swala ndi kupereka Zakaat uku ali odzichepetsa. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 5

وَمَن يَتَوَلَّ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فَإِنَّ حِزۡبَ ٱللَّهِ هُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ

Ndipo amene achite Allah ndi Mtumiki Wake, ndi omwe akhulupirira kukhala atetezi ake, (ndithu iwo ndi a chipani cha Allah). Ndithu chipani cha Allah ndicho chopambana. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَكُمۡ هُزُوٗا وَلَعِبٗا مِّنَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكُمۡ وَٱلۡكُفَّارَ أَوۡلِيَآءَۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Musapalane nawo ubwenzi omwe akuchichitira chipongwe ndi masewera Chipembedzo chanu mwa omwe apatsidwa mabuku patsogolo panu, ndiponso mwa osakhulupirira, ndipo opani Allah ngati inu mulidi okhulupirira. info
التفاسير: