แปล​ความหมาย​อัลกุรอาน​ - คำแปลภาษาชิเชวา - โดยคอลิด อิบรอฮีม เบตาลา

หมายเลข​หน้า​:close

external-link copy
60 : 6

وَهُوَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُم بِٱلَّيۡلِ وَيَعۡلَمُ مَا جَرَحۡتُم بِٱلنَّهَارِ ثُمَّ يَبۡعَثُكُمۡ فِيهِ لِيُقۡضَىٰٓ أَجَلٞ مُّسَمّٗىۖ ثُمَّ إِلَيۡهِ مَرۡجِعُكُمۡ ثُمَّ يُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Iye ndiyemwe amakupatsani imfa (yatulo) nthawi yausiku, ndipo amadziwa zimene mwachita masana, kenako amakudzutsani mmenemo kuti ikwane nthawi yanu yoikidwa (yofera); kenako kwa Iye ndiko kobwerera kwanu, nadzakuuzani zimene munkachita. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 6

وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۖ وَيُرۡسِلُ عَلَيۡكُمۡ حَفَظَةً حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ تَوَفَّتۡهُ رُسُلُنَا وَهُمۡ لَا يُفَرِّطُونَ

Iye ndi M’gonjesi pa akapolo Ake ndipo amakutumizirani (angelo) osunga, (olemba zochita zanu); kufikira mmodzi wanu imfa ikamdzera, angelo athuwo amampatsa imfa, ndipo iwo sanyozera (ntchito yawo). info
التفاسير:

external-link copy
62 : 6

ثُمَّ رُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۚ أَلَا لَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَهُوَ أَسۡرَعُ ٱلۡحَٰسِبِينَ

Kenako adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona. Dziwani kuti kuweruza Nkwake. Iye Ngwachangu powerengera kuposa owerengera (onse). info
التفاسير:

external-link copy
63 : 6

قُلۡ مَن يُنَجِّيكُم مِّن ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ تَدۡعُونَهُۥ تَضَرُّعٗا وَخُفۡيَةٗ لَّئِنۡ أَنجَىٰنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ

Nena: “Kodi ndani amakupulumutsani m’masautso a pamtunda ndi panyanja?” Mumampempha modzichepetsa ndi motsitsa mawu (kuti): “Ngati atipulumutsa m’mazunzo awa, ndithudi tidzakhala mwa othokoza.” info
التفاسير:

external-link copy
64 : 6

قُلِ ٱللَّهُ يُنَجِّيكُم مِّنۡهَا وَمِن كُلِّ كَرۡبٖ ثُمَّ أَنتُمۡ تُشۡرِكُونَ

Nena: “Allah ndi Yemwe amakupulumutsani ku zimenezo ndi ku masautso a mtundu uliwonse. Kenako inu mukumphatikiza ndi mafano. info
التفاسير:

external-link copy
65 : 6

قُلۡ هُوَ ٱلۡقَادِرُ عَلَىٰٓ أَن يَبۡعَثَ عَلَيۡكُمۡ عَذَابٗا مِّن فَوۡقِكُمۡ أَوۡ مِن تَحۡتِ أَرۡجُلِكُمۡ أَوۡ يَلۡبِسَكُمۡ شِيَعٗا وَيُذِيقَ بَعۡضَكُم بَأۡسَ بَعۡضٍۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَفۡقَهُونَ

Nena: “Iye Ngokhoza kukutumizirani chilango kuchokera pamwamba panu kapena pansi pa miyendo yanu, kapena kudzetsa chisokonezo nkukhala magulumagulu (osamvana), ndipo (akhoza) kuwalawitsa ena a inu chilango cha mtopola wa ena.” Taona momwe tikufotokozera zizindikiro kuti iwo azindikire. info
التفاسير:

external-link copy
66 : 6

وَكَذَّبَ بِهِۦ قَوۡمُكَ وَهُوَ ٱلۡحَقُّۚ قُل لَّسۡتُ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٖ

Koma anthu ako aitsutsa iyo (Qur’an) pomwe ili yoona. Nena: “Ine sindili muyang’anili pa inu.” info
التفاسير:

external-link copy
67 : 6

لِّكُلِّ نَبَإٖ مُّسۡتَقَرّٞۚ وَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Nkhani iliyonse (yomwe yatchulidwa apa) ili ndi nthawi yake yodziwika (yofikira). Ndipo posachedwapa mudziwa (izi). info
التفاسير:

external-link copy
68 : 6

وَإِذَا رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ يَخُوضُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ يَخُوضُواْ فِي حَدِيثٍ غَيۡرِهِۦۚ وَإِمَّا يُنسِيَنَّكَ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَلَا تَقۡعُدۡ بَعۡدَ ٱلذِّكۡرَىٰ مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo (iwe Msilamu weniweni) ukawaona omwe akuchita chipongwe ndi Ayah Zathu, apatuke mpaka anene nkhani ina. Ndipo ngati satana atakuiwalitsa, (nkukhala nawo pomwe iwo akukambirana zotere), choncho, pambuyo pokumbukira usakhale pamodzi ndi anthu ochita zoipa. info
التفاسير: