[335] Anthu am’mudzi wa Saba’a komwe nkudziko la Yemeni, Allah adawapatsa madalitso ambiri pamene iwo amatsatira malamuio Ake ndi kumthokoza. Adawadalitsa ndi minda ya zipatso zokoma zomwe zidalibe nyengo yeniyeni yobalira, kotero kuti azimayi ankangosenza madengu nkumangoyenda pansi pa mitengo ndipo mwadzidzidzi ankangoona madengu ali odzaza ndi zipatso zoyoyoka m’mitengoyo. Koma pamene adasiya kumuyamika Allah ndi kutsatira malamulo Ake, adawaonongera mindayo ndi chigumula ndi kuwasinthitsira zipatso zawo ndi zipatso zopanda pake.