[333] Allah Wapamwambamwamba adamfewetsera Daud chitsulo kotero kuti adachisungunula nkusanduka ngati phala, napanga kuchokera m’phala limenelo zovala zodzitetezera pa nkhondo, ndiponso ziwiya zina zothandiza pa umoyo. Ichi chidali chisomo chachikulu chimene Allah adamdalitsa nacho iye pamodzi ndi ife tonse.
[334] Kalelo anthu adali ndi chikhulupiliro chakuti ziwanda zimadziwa zamseri; monga kudziwa zam’tsogolo. Ndipo kudapezeka kuti Sulaiman adaimilira kupemphera ku chipinda chake chopemphelera uku atatsamira ndodo yake, imfa niimpeza ali chiimilire, choncho adakhala chaka chathunthu ali chomwecho uku atafa kale. Mmenemo nkuti ziwanda zikugwira ntchito yotopetsa, osadziwa kuti Sulaiman adafa, mpaka pamene chiswe chidadya ndodo imene adatsamira, nagwa pansi. Apo mpomwe imfa yake idadziwika. Potero anthu adadziwa tsopano kuti ziwanda sizidziwa zam’tsogolo.