แปล​ความหมาย​อัลกุรอาน​ - คำแปลภาษาชิเชวา - โดยคอลิด อิบรอฮีม เบตาลา

หมายเลข​หน้า​:close

external-link copy
36 : 27

فَلَمَّا جَآءَ سُلَيۡمَٰنَ قَالَ أَتُمِدُّونَنِ بِمَالٖ فَمَآ ءَاتَىٰنِۦَ ٱللَّهُ خَيۡرٞ مِّمَّآ ءَاتَىٰكُمۚ بَلۡ أَنتُم بِهَدِيَّتِكُمۡ تَفۡرَحُونَ

Choncho pamene adafika (wamthenga wamkulu) kwa Sulaiman (ndi kupereka mphatso zija, Sulaiman adazikana) nati: “Mukundithandiza ndi chuma? zimene Allah wandipatsa ndizabwino kuposa zimene wakupatsani. Koma inu mukusangalala ndi mphatso zanu.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 27

ٱرۡجِعۡ إِلَيۡهِمۡ فَلَنَأۡتِيَنَّهُم بِجُنُودٖ لَّا قِبَلَ لَهُم بِهَا وَلَنُخۡرِجَنَّهُم مِّنۡهَآ أَذِلَّةٗ وَهُمۡ صَٰغِرُونَ

Bwerera (nazo) kwa iwo; ndithu tiwadzera ndi gulu lankhondo lomwe iwo sangathe kulimbana nalo; mtheradi, tikawatulutsa m’menemo ali onyozeka ndi oyaluka.” info
التفاسير:

external-link copy
38 : 27

قَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَيُّكُمۡ يَأۡتِينِي بِعَرۡشِهَا قَبۡلَ أَن يَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ

(Sulaiman adasonkhanitsa nduna zake) nati: “E inu nduna! Ndani abwere ndi mpando wake wachifumuwo kwa ine asadandidzere ali ogonja?” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 27

قَالَ عِفۡرِيتٞ مِّنَ ٱلۡجِنِّ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن تَقُومَ مِن مَّقَامِكَۖ وَإِنِّي عَلَيۡهِ لَقَوِيٌّ أَمِينٞ

Chiwanda chotchedwa Ifrit chidati: “Ine ndikubweletsera chimenecho usadaimilire pamalo ako (oweruzira). Ndipo ndithu ine pa icho (chimpando) ndine wanyonga, wokhulupirika.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 27

قَالَ ٱلَّذِي عِندَهُۥ عِلۡمٞ مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن يَرۡتَدَّ إِلَيۡكَ طَرۡفُكَۚ فَلَمَّا رَءَاهُ مُسۡتَقِرًّا عِندَهُۥ قَالَ هَٰذَا مِن فَضۡلِ رَبِّي لِيَبۡلُوَنِيٓ ءَأَشۡكُرُ أَمۡ أَكۡفُرُۖ وَمَن شَكَرَ فَإِنَّمَا يَشۡكُرُ لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ رَبِّي غَنِيّٞ كَرِيمٞ

Yemwe adali ndi maphunziro (akuya) a m’buku adati: “Ine ndikubweletsera (chimpandocho) maso ako asadaphetire (usadatsinzine ndi kupenya).” Pamene adachiona chitakhazikitsidwa patsogolo pake, adati: “Izi nchifukwa cha ufulu wa Mbuye wanga kuti andiyese mayeso kodi ndithokoza kapena ndiusuliza (ufulu Wake). Ndipo amene akuthokoza ndithu ubwino wa kuthokozako udzakhala pa iye mwini. Ndipo amene akukana (mtendere wa Allah posathokoza), ndithu Mbuye wanga Ngokhupuka; Waulemu, (sasaukira chilichonse kwa anthu).” info
التفاسير:

external-link copy
41 : 27

قَالَ نَكِّرُواْ لَهَا عَرۡشَهَا نَنظُرۡ أَتَهۡتَدِيٓ أَمۡ تَكُونُ مِنَ ٱلَّذِينَ لَا يَهۡتَدُونَ

(Sulaiman) adati: “Msinthireni (maonekedwe a) mpando wake wachifumuwo kuti tione kodi auzindikira kapena akhala mwa omwe sazindikira (chinthu). info
التفاسير:

external-link copy
42 : 27

فَلَمَّا جَآءَتۡ قِيلَ أَهَٰكَذَا عَرۡشُكِۖ قَالَتۡ كَأَنَّهُۥ هُوَۚ وَأُوتِينَا ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهَا وَكُنَّا مُسۡلِمِينَ

Choncho pamene (mfumukazi) idadza, kudanenedwa: “Kodi mpando wako wachifumu uli ngati uwu?” Idati: “Uli ngati umenewu, ndithu ndipo ife tidapatsidwa kuzindikira (za uneneri wanu) tisadaone chozizwitsa ichi; ndipo, ndithu tidadzipereka (kwa Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
43 : 27

وَصَدَّهَا مَا كَانَت تَّعۡبُدُ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ إِنَّهَا كَانَتۡ مِن قَوۡمٖ كَٰفِرِينَ

Ndipo (Sulaiman) adamuletsa zomwe amazipembedza kusiya Allah. Ndithu (mfumukaziyo) idali mwa anthu osakhulupirira (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 27

قِيلَ لَهَا ٱدۡخُلِي ٱلصَّرۡحَۖ فَلَمَّا رَأَتۡهُ حَسِبَتۡهُ لُجَّةٗ وَكَشَفَتۡ عَن سَاقَيۡهَاۚ قَالَ إِنَّهُۥ صَرۡحٞ مُّمَرَّدٞ مِّن قَوَارِيرَۗ قَالَتۡ رَبِّ إِنِّي ظَلَمۡتُ نَفۡسِي وَأَسۡلَمۡتُ مَعَ سُلَيۡمَٰنَ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

(Mfumukazi ija) idauzidwa kuti: “Lowa mkhonde la nyumba.” Koma pamene adaliona adaliganizira kuti ndidziwe; adakweza nsalu kumiyendo yake. (Sulaiman) adati: “Ndithu limeneli ndikhonde lomwe laziridwa ndi magalasi.” (Mfumukazi) idati: “E Mbuye wanga! Ndadzichitira ndekha chinyengo; choncho, ndagonjera kwa Allah, Mbuye wazolengedwa pamodzi ndi Sulaiman.” info
التفاسير: