แปล​ความหมาย​อัลกุรอาน​ - คำแปลภาษาชิเชวา - โดยคอลิด อิบรอฮีม เบตาลา

หมายเลข​หน้า​:close

external-link copy
28 : 24

فَإِن لَّمۡ تَجِدُواْ فِيهَآ أَحَدٗا فَلَا تَدۡخُلُوهَا حَتَّىٰ يُؤۡذَنَ لَكُمۡۖ وَإِن قِيلَ لَكُمُ ٱرۡجِعُواْ فَٱرۡجِعُواْۖ هُوَ أَزۡكَىٰ لَكُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِيمٞ

Koma ngati simupeza munthu aliyense m’menemo, musalowe kufikira mutapatsidwa chilolezo. Ndipo mukauzidwa kuti: “Bwererani.” Bwererani; chimenechi nchokuyeretsani. Ndipo Allah akudziwa zimene muchita. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 24

لَّيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَدۡخُلُواْ بُيُوتًا غَيۡرَ مَسۡكُونَةٖ فِيهَا مَتَٰعٞ لَّكُمۡۚ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تُبۡدُونَ وَمَا تَكۡتُمُونَ

Sikulakwa kwa inu kulowa m’nyumba zosakhalidwa, (monga sitolo, hotela; popanda chilolezo), momwe muli zokuthandizani; ndipo Allah akudziwa zomwe mukuonetsera poyera ndi zimene mukubisa. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 24

قُل لِّلۡمُؤۡمِنِينَ يَغُضُّواْ مِنۡ أَبۡصَٰرِهِمۡ وَيَحۡفَظُواْ فُرُوجَهُمۡۚ ذَٰلِكَ أَزۡكَىٰ لَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ خَبِيرُۢ بِمَا يَصۡنَعُونَ

Auze okhulupirira achimuna kuti adzolitse maso awo (asayang’ane zoletsedwa), ndipo asunge umaliseche wawo. Ichi nchoyera kwambiri kwa iwo. Ndithu Allah akudziwa nkhani za zonse zomwe achita. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 24

وَقُل لِّلۡمُؤۡمِنَٰتِ يَغۡضُضۡنَ مِنۡ أَبۡصَٰرِهِنَّ وَيَحۡفَظۡنَ فُرُوجَهُنَّ وَلَا يُبۡدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا مَا ظَهَرَ مِنۡهَاۖ وَلۡيَضۡرِبۡنَ بِخُمُرِهِنَّ عَلَىٰ جُيُوبِهِنَّۖ وَلَا يُبۡدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا لِبُعُولَتِهِنَّ أَوۡ ءَابَآئِهِنَّ أَوۡ ءَابَآءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوۡ أَبۡنَآئِهِنَّ أَوۡ أَبۡنَآءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوۡ إِخۡوَٰنِهِنَّ أَوۡ بَنِيٓ إِخۡوَٰنِهِنَّ أَوۡ بَنِيٓ أَخَوَٰتِهِنَّ أَوۡ نِسَآئِهِنَّ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُنَّ أَوِ ٱلتَّٰبِعِينَ غَيۡرِ أُوْلِي ٱلۡإِرۡبَةِ مِنَ ٱلرِّجَالِ أَوِ ٱلطِّفۡلِ ٱلَّذِينَ لَمۡ يَظۡهَرُواْ عَلَىٰ عَوۡرَٰتِ ٱلنِّسَآءِۖ وَلَا يَضۡرِبۡنَ بِأَرۡجُلِهِنَّ لِيُعۡلَمَ مَا يُخۡفِينَ مِن زِينَتِهِنَّۚ وَتُوبُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ جَمِيعًا أَيُّهَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

Ndipo auze okhulupirira achikazi kuti adzolitse maso awo, ndikusunga umaliseche wawo, ndipo asaonetse (poyera) zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo; ndipo asaonetse poyera zodzikongoletsa nazo koma kwa amuna awo, kapena atate awo, kapena apongozi awo, kapena ana awo, kapena ana a amuna awo, kapena abale awo, kapena ana a abale awo, kapena ana a alongo awo, kapena akazi anzawo (achisilamu). Kapena yemwe wapatidwa ndi dzanja lamanja (monga kapolo), kapena otsatira (antchito) omwe ndi amuna opanda zilakolako za akazi ndi ana omwe sadziwa za akazi. Ndipo asamenyetse miyendo yawo (pansi) kuti zidziwike zimene akubisa mwa zomwe amadzikongoletsa nazo. Ndipo tembenukirani kwa Allah, nonse inu okhulupirira kuti mupambane. info
التفاسير: