แปล​ความหมาย​อัลกุรอาน​ - คำแปลภาษาชิเชวา - โดยคอลิด อิบรอฮีม เบตาลา

Ibrâhîm

external-link copy
1 : 14

الٓرۚ كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ إِلَيۡكَ لِتُخۡرِجَ ٱلنَّاسَ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِ بِإِذۡنِ رَبِّهِمۡ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ

Alif-Lâm-Ra. (Ili ndi) buku lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti uwatulutse anthu mu mdima ndi kuwaika mkuunika - mwalamulo la Mbuye wawo - uwapititse kunjira ya Mwini mphamvu zoposa, Woyamikidwa. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 14

ٱللَّهِ ٱلَّذِي لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَوَيۡلٞ لِّلۡكَٰفِرِينَ مِنۡ عَذَابٖ شَدِيدٍ

Allah, Yemwe ndi Zake zonse zakumwamba ndi pansi. Ndipo kuonongeka ndi chilango chokhwima kudzatsimikizika pa osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 14

ٱلَّذِينَ يَسۡتَحِبُّونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا عَلَى ٱلۡأٓخِرَةِ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٖ

Amene akukondetsa moyo wadziko lapansi kuposa moyo wa pambuyo pa imfa, ndipo amatsekereza (anthu) ku njira ya Allah ndikufuna kuikhotetsa (pomwe njirayo njosakhota). Iwo ali mkusokera kotalikana kwambiri (ndi choonadi). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 14

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا بِلِسَانِ قَوۡمِهِۦ لِيُبَيِّنَ لَهُمۡۖ فَيُضِلُّ ٱللَّهُ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Ndipo sitidamtume mtumiki aliyense koma ndi chiyankhulo cha anthu ake kuti awafotokozere. Kenako Allah akumsiya kusokera amene wamfuna (chifukwa mwini wake safuna kuongoka). Ndipo amamuongolera yemwe wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 14

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ أَنۡ أَخۡرِجۡ قَوۡمَكَ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِ وَذَكِّرۡهُم بِأَيَّىٰمِ ٱللَّهِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٖ

Ndipo ndithu tidamtumiza Mûsa ndi zozizwitsa Zathu (tidamuuza): “Achotse anthu ako mu mdima (wa umbuli) ndi kuwaika mkuunika (kwa chikhulupiliro) ndipo uwakumbutse masiku a Allah (a masautso).” Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa yense wopirira, wothokoza. info
التفاسير: