Përkthimi i kuptimeve të Kuranit Fisnik - Përkthimi çiçevë - Khalid Ibrahim Betiala

Al-Wâqi’ah

external-link copy
1 : 56

إِذَا وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ

Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 56

لَيۡسَ لِوَقۡعَتِهَا كَاذِبَةٌ

Palibe wotsutsa za kuchitika kwake. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 56

خَافِضَةٞ رَّافِعَةٌ

Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 56

إِذَا رُجَّتِ ٱلۡأَرۡضُ رَجّٗا

Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 56

وَبُسَّتِ ٱلۡجِبَالُ بَسّٗا

Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 56

فَكَانَتۡ هَبَآءٗ مُّنۢبَثّٗا

Nkukhala fumbi longouluka. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 56

وَكُنتُمۡ أَزۡوَٰجٗا ثَلَٰثَةٗ

Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 56

فَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ

Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja! info
التفاسير:

external-link copy
9 : 56

وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ

Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere! info
التفاسير:

external-link copy
10 : 56

وَٱلسَّٰبِقُونَ ٱلسَّٰبِقُونَ

Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 56

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡمُقَرَّبُونَ

Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 56

فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

M’minda yamtendere. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 56

ثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ

(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 56

وَقَلِيلٞ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ

Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 56

عَلَىٰ سُرُرٖ مَّوۡضُونَةٖ

Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide, info
التفاسير:

external-link copy
16 : 56

مُّتَّكِـِٔينَ عَلَيۡهَا مُتَقَٰبِلِينَ

Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi). info
التفاسير: