[292] Osakhulupilira amumzinda wa Makka adali kuinyoza Qur’an namati ndi buku labodza limene walipeka yekhayekha Muhammad (s.a.w) ndikumamnamizira Allah kuti ndiye walivumbulutsa. Amatinso anthu a mabuku ndiwo adamthandiza kulipeka. Zonena zawozi nzabodza zokhazokha chifukwa Qur’an yomwe Muhammad (s.a.w) akuiwerengayo ili m’Charabu osati m’Chiyuda.
[293] Amamunenera zachipongwe Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti: “Nchiyani watiposa uyu pamene akudzitcha yekha kuti ndi Mtumiki? lye akudya chakudya monga momwe ife tidyera, ndipo akuyendayenda m’misika kunka nafunafuna zokhalira moyo monga anthu ena onse achitira. Akadakhaladi Mtumiki ndiye kuti Allah akadampatsa zosowa zake zonse. Ngati alidi Mtumiki bwanji Allah sadamtsitsire angelo kumwamba kuti azimthandiza? Zikadatero apo tikadamkhulupilira.’’