Përkthimi i kuptimeve të Kuranit Fisnik - Përkthimi çiçevë - Khalid Ibrahim Betiala

Numri i faqes:close

external-link copy
94 : 2

قُلۡ إِن كَانَتۡ لَكُمُ ٱلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ ٱللَّهِ خَالِصَةٗ مِّن دُونِ ٱلنَّاسِ فَتَمَنَّوُاْ ٱلۡمَوۡتَ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Auze (Ayudawo): “Ngati nyumba yomaliza kwa Allah njanu nokha, osati anthu ena (monga momwe mukunenera), ilakalakeni imfa ngati mukunenadi zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
95 : 2

وَلَن يَتَمَنَّوۡهُ أَبَدَۢا بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِٱلظَّٰلِمِينَ

Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa. info
التفاسير:

external-link copy
96 : 2

وَلَتَجِدَنَّهُمۡ أَحۡرَصَ ٱلنَّاسِ عَلَىٰ حَيَوٰةٖ وَمِنَ ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْۚ يَوَدُّ أَحَدُهُمۡ لَوۡ يُعَمَّرُ أَلۡفَ سَنَةٖ وَمَا هُوَ بِمُزَحۡزِحِهِۦ مِنَ ٱلۡعَذَابِ أَن يُعَمَّرَۗ وَٱللَّهُ بَصِيرُۢ بِمَا يَعۡمَلُونَ

Ndipo muwapeza (Ayuda) kuti ngokondetsetsa kukhala ndi moyo wautali kuposa anthu ena, kuposanso anthu amene akuphatikiza (Allah ndi mafano). Aliyense wa iwo amafuna atapatsidwa moyo wokwana zaka chikwi chimodzi. Pomwe kupatsidwa kwake moyo wautali sikungamuike kutali ndi chilango. Ndipo Allah akuona zonse zimene akuchita. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 2

قُلۡ مَن كَانَ عَدُوّٗا لِّـجِبۡرِيلَ فَإِنَّهُۥ نَزَّلَهُۥ عَلَىٰ قَلۡبِكَ بِإِذۡنِ ٱللَّهِ مُصَدِّقٗا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَهُدٗى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ

Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
98 : 2

مَن كَانَ عَدُوّٗا لِّلَّهِ وَمَلَٰٓئِكَتِهِۦ وَرُسُلِهِۦ وَجِبۡرِيلَ وَمِيكَىٰلَ فَإِنَّ ٱللَّهَ عَدُوّٞ لِّلۡكَٰفِرِينَ

Amene ali mdani wa Allah, angelo Ake, atumiki Ake, Gaburieli ndi Mikayeli, ndithu Allah ndi mdani wa osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
99 : 2

وَلَقَدۡ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖۖ وَمَا يَكۡفُرُ بِهَآ إِلَّا ٱلۡفَٰسِقُونَ

Ndithu tavumbulutsa kwa iwe zisonyezo zoonekera. Ndipo palibe wozikana koma okhawo opandukira chilamulo cha Allah. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 2

أَوَكُلَّمَا عَٰهَدُواْ عَهۡدٗا نَّبَذَهُۥ فَرِيقٞ مِّنۡهُمۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Kodi sizili tero kuti panthawi iliyonse akupangana pangano lamphamvu, ena aiwo akulitaya? Koma ambiri aiwo sakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
101 : 2

وَلَمَّا جَآءَهُمۡ رَسُولٞ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُصَدِّقٞ لِّمَا مَعَهُمۡ نَبَذَ فَرِيقٞ مِّنَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ كِتَٰبَ ٱللَّهِ وَرَآءَ ظُهُورِهِمۡ كَأَنَّهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo pamene (Ayuda) adawadzera Mtumiki wochokera kwa Allah uku akutsimikidzira chomwe iwo ali nacho, gulu lina mwa omwe adapatsidwa buku adataya buku la Allah kumbuyo kwa misana yawo ngati kuti sakulidziwa. info
التفاسير: