[482] Kujeda kwa mtundu uliwonse ndi koipa. Anthu ambiri amaganiza kuti kujeda ndi chinthu chochepa, saona kuti ndi chinthu choipa, pomwe Qur’an ikuletsa kwatunthu mpaka mwakuti imamufanizira munthu wojeda ngati munthu yemwe amadya minofu ya mnzake wakufa. Mu Ayah imeneyi, Allah wanena kuti “Wayilun” lomwe tanthauzo lake ndi “Kuonongeka koopsa.” Choncho nkofunika kwa munthu aliyense kupewa khalidwe lojeda.
[483] Mmenemo ndi momwe alili munthu wa umbombo, kukoma kwa chuma kwa iye, ndikuchisonkhanitsa ndikumachiwerengera akakhala ndi danga; sikuti akufuna kudziwa kuchuluka kwake koma kungokondweretsedwa ndikuchiwerengako. Saganizira zimene zingamuthandize iye mwini kapena kuthandiza anzake.
Chuma ntchito yake ndikuti chimthandize mwini chumacho pa zinthu zabwino zosiyanasiyana pamodzi ndi anzake, osati kungochikhazika ndikumangochiwerengera mokhumbiza ena.