Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Al-Ghâshiyah

external-link copy
1 : 88

هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡغَٰشِيَةِ

Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)? info
التفاسير:

external-link copy
2 : 88

وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٍ خَٰشِعَةٌ

Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,[425] info

[425] Tanthauzo la nkhope apa ndi eni nkhopezo. Amene akunenedwa pamenepa ndi anthu oipa. Allah watchula nkhope chifukwa ndi chiwalo cholemekezeka pa chilengedwe cha munthu ndipo ndi pamene pali chithunzi chake.

التفاسير:

external-link copy
3 : 88

عَامِلَةٞ نَّاصِبَةٞ

Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 88

تَصۡلَىٰ نَارًا حَامِيَةٗ

Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 88

تُسۡقَىٰ مِنۡ عَيۡنٍ ءَانِيَةٖ

Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 88

لَّيۡسَ لَهُمۡ طَعَامٌ إِلَّا مِن ضَرِيعٖ

Sadzakhala ndichakudya koma minga. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 88

لَّا يُسۡمِنُ وَلَا يُغۡنِي مِن جُوعٖ

Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 88

وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ نَّاعِمَةٞ

Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 88

لِّسَعۡيِهَا رَاضِيَةٞ

Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).[426] info

[426] Tanthauzo la “kukondweretsedwa ndi zochita zawo’’ ndikuti anthu abwino adzakondwera ndi ntchito zawo zabwino zomwe adazichita pa dziko lapansi akadzakhala ndi malipiro abwino pa tsiku lachimaliziro.

التفاسير:

external-link copy
10 : 88

فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ

M’minda ya pamwamba (Jannah). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 88

لَّا تَسۡمَعُ فِيهَا لَٰغِيَةٗ

Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 88

فِيهَا عَيۡنٞ جَارِيَةٞ

Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).[427] info

[427] (Ndime 12-16) Zosangalatsa zenizeni za tsiku lachimaliziro monga momwe adatiuzira Mneneri (s.a.w) kuti ku Jannah kuli zinthu zimene diso silidapenyepo ngakhale khutu silidamvepo ndipo sizidapitepo m’maganizo a munthu. Choncho zokondweretsa izi zimene Allah watiuza apa akungofanizira ndi zinthu zomwe tikuzidziwa.

التفاسير:

external-link copy
13 : 88

فِيهَا سُرُرٞ مَّرۡفُوعَةٞ

Mmenemo muli makama a pamwamba, info
التفاسير:

external-link copy
14 : 88

وَأَكۡوَابٞ مَّوۡضُوعَةٞ

Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo), info
التفاسير:

external-link copy
15 : 88

وَنَمَارِقُ مَصۡفُوفَةٞ

Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere info
التفاسير:

external-link copy
16 : 88

وَزَرَابِيُّ مَبۡثُوثَةٌ

Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 88

أَفَلَا يَنظُرُونَ إِلَى ٱلۡإِبِلِ كَيۡفَ خُلِقَتۡ

Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?[428] info

[428] (Ndime 17-20) Allah akuwauza kuti ayang’ane chilengedwe cha ngamira, thambo, mapiri ndi nthaka. Pambuyo pake alingalire, aone kuti amene adalenga zimenezo ngotha kuchita chilichonse monga kuukitsa anthu m’manda. Cholinga cha Allah potchula zinthu zimenezi, ngakhale kuti malangizowa nga munthu aliyense, koma adali kuwauza akafiri a pa Makka amene zinthu zimenezi maso awo ankaziona nthawi ndi nthawi.

التفاسير:

external-link copy
18 : 88

وَإِلَى ٱلسَّمَآءِ كَيۡفَ رُفِعَتۡ

Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)? info
التفاسير:

external-link copy
19 : 88

وَإِلَى ٱلۡجِبَالِ كَيۡفَ نُصِبَتۡ

Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)? info
التفاسير:

external-link copy
20 : 88

وَإِلَى ٱلۡأَرۡضِ كَيۡفَ سُطِحَتۡ

Ndi nthaka momwe idayalidwira. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 88

فَذَكِّرۡ إِنَّمَآ أَنتَ مُذَكِّرٞ

Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 88

لَّسۡتَ عَلَيۡهِم بِمُصَيۡطِرٍ

Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).[429] info

[429] Ayah iyi ikukwana kuwatsutsa adani a Chisilamu amene akunena kuti, “chipembedzo cha Chisilamu chidafala ndi lupanga.” Kutanthauza kuti ankawakakamiza anthu kuti achivomere chipembedzochi. Sichodabwitsa kuona adani a Chisilamu akuchinyoza chipembedzochi, koma chodabwitsa nchakuti mawu onamawa nkumatulukanso mkamwa mwa anthu omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu. Nzoona alipo ena mwa anthu odziwa za chipembedzo (ma Ulama) amene adanena kuti chipembedzo cha Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga. Koma simonga momwe akutanthauzilira adani amene sadziwa za Chisilamu nkumangotsatira mabodza a akuluakulu awo. Cholinga cha ma Ulama ponena kuti “Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga” kumeneko ndi kudziteteza kwa adani omwe adafuna kuchithetsa, osati kuwakakamiza anthu kulowa mchipembedzo. Kukakamiza anthu kulowa mChisilamu nkosaloledwa. Amene akudziwa mbiri ya Chisilamu, akudziwa kuti Asilamu sadalamulidwe kuchita Jihâd mpaka pamene akafiri adali kuwazunza. Pali nkhani zambiri za Maswahaba (otsatira Mneneri) (s.a.w) ku Madina pamene adafuna kuwakakamiza ana awo kulowa m’Chisilamu, koma Mneneri adawakaniza kutero. Basi, munthu amene akunena zoterezo mwina akutero pa chifukwa chosadziwa za chipembedzo cha Chisilamu, mwinanso nkukhala misala basi.

التفاسير:

external-link copy
23 : 88

إِلَّا مَن تَوَلَّىٰ وَكَفَرَ

Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako), info
التفاسير:

external-link copy
24 : 88

فَيُعَذِّبُهُ ٱللَّهُ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَكۡبَرَ

Allah amulanga chilango chachikulu zedi. info
التفاسير:

external-link copy
25 : 88

إِنَّ إِلَيۡنَآ إِيَابَهُمۡ

Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 88

ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا حِسَابَهُم

Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife. info
التفاسير: