[425] Tanthauzo la nkhope apa ndi eni nkhopezo. Amene akunenedwa pamenepa ndi anthu oipa. Allah watchula nkhope chifukwa ndi chiwalo cholemekezeka pa chilengedwe cha munthu ndipo ndi pamene pali chithunzi chake.
[426] Tanthauzo la “kukondweretsedwa ndi zochita zawo’’ ndikuti anthu abwino adzakondwera ndi ntchito zawo zabwino zomwe adazichita pa dziko lapansi akadzakhala ndi malipiro abwino pa tsiku lachimaliziro.
[427] (Ndime 12-16) Zosangalatsa zenizeni za tsiku lachimaliziro monga momwe adatiuzira Mneneri (s.a.w) kuti ku Jannah kuli zinthu zimene diso silidapenyepo ngakhale khutu silidamvepo ndipo sizidapitepo m’maganizo a munthu. Choncho zokondweretsa izi zimene Allah watiuza apa akungofanizira ndi zinthu zomwe tikuzidziwa.
[428] (Ndime 17-20) Allah akuwauza kuti ayang’ane chilengedwe cha ngamira, thambo, mapiri ndi nthaka. Pambuyo pake alingalire, aone kuti amene adalenga zimenezo ngotha kuchita chilichonse monga kuukitsa anthu m’manda. Cholinga cha Allah potchula zinthu zimenezi, ngakhale kuti malangizowa nga munthu aliyense, koma adali kuwauza akafiri a pa Makka amene zinthu zimenezi maso awo ankaziona nthawi ndi nthawi.
[429] Ayah iyi ikukwana kuwatsutsa adani a Chisilamu amene akunena kuti, “chipembedzo cha Chisilamu chidafala ndi lupanga.” Kutanthauza kuti ankawakakamiza anthu kuti achivomere chipembedzochi. Sichodabwitsa kuona adani a Chisilamu akuchinyoza chipembedzochi, koma chodabwitsa nchakuti mawu onamawa nkumatulukanso mkamwa mwa anthu omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu. Nzoona alipo ena mwa anthu odziwa za chipembedzo (ma Ulama) amene adanena kuti chipembedzo cha Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga. Koma simonga momwe akutanthauzilira adani amene sadziwa za Chisilamu nkumangotsatira mabodza a akuluakulu awo. Cholinga cha ma Ulama ponena kuti “Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga” kumeneko ndi kudziteteza kwa adani omwe adafuna kuchithetsa, osati kuwakakamiza anthu kulowa mchipembedzo. Kukakamiza anthu kulowa mChisilamu nkosaloledwa. Amene akudziwa mbiri ya Chisilamu, akudziwa kuti Asilamu sadalamulidwe kuchita Jihâd mpaka pamene akafiri adali kuwazunza. Pali nkhani zambiri za Maswahaba (otsatira Mneneri) (s.a.w) ku Madina pamene adafuna kuwakakamiza ana awo kulowa m’Chisilamu, koma Mneneri adawakaniza kutero. Basi, munthu amene akunena zoterezo mwina akutero pa chifukwa chosadziwa za chipembedzo cha Chisilamu, mwinanso nkukhala misala basi.