Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

external-link copy
34 : 8

وَمَا لَهُمۡ أَلَّا يُعَذِّبَهُمُ ٱللَّهُ وَهُمۡ يَصُدُّونَ عَنِ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ وَمَا كَانُوٓاْ أَوۡلِيَآءَهُۥٓۚ إِنۡ أَوۡلِيَآؤُهُۥٓ إِلَّا ٱلۡمُتَّقُونَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

(Kodi iwo Aquraish) ali ndi chinthu chanji (chabwino chimene) chingamuletse Allah kuwalanga? Pomwe iwo akuwatsekereza anthu kulowa mu Msikiti Wopatulika. Iwo sanayenere kukhala ouyang’anira (Msikitiwo). Palibe angauyang’anire koma olungama, koma anthu ambiri sadziwa.[201] info

[201] M’chaka chachisanu nchimodzi (6) chakusamuka, Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi omtsatira ake ochuluka zedi adapita ku Makka ncholinga chokachita mapemphero a Umra. Koma Aquraish adamuletsa kulowa mu mzinda wa Makka podziganizira kuti iwo ndiwo oyang’anira Kaaba.

التفاسير: