Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Al-Mujadilah

external-link copy
1 : 58

قَدۡ سَمِعَ ٱللَّهُ قَوۡلَ ٱلَّتِي تُجَٰدِلُكَ فِي زَوۡجِهَا وَتَشۡتَكِيٓ إِلَى ٱللَّهِ وَٱللَّهُ يَسۡمَعُ تَحَاوُرَكُمَآۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٌ

۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse).[347] info

[347] Arabu adali ndi chizolowezi chakupatukana ndi mkazi ponena mawu akuti: “Ndikukuyerekeza ngati mayi wanga.” Choncho amangokhala naye mkazi uja, osamkhudza ndiponso osamulola kuti akwatiwe ndi mwamuna wina. Samamchitiranso zimene munthu amachitira mkazi wake monga kumveka ndi kumdyetsa. Msilamu wina adamsiya mkazi masiyidwe onga amenewa ndipo mkazi uja adapita kukakambirana naye Mtumiki (s.a.w). Choncho Chisilamu chidaletsa machitidwe onga amenewa.

التفاسير: