Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Número de página:close

external-link copy
182 : 2

فَمَنۡ خَافَ مِن مُّوصٖ جَنَفًا أَوۡ إِثۡمٗا فَأَصۡلَحَ بَيۡنَهُمۡ فَلَآ إِثۡمَ عَلَيۡهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Ndipo amene waopa kuti wopereka wasiya angapendekere kumbali yokhota kapena ku uchimo, nalinganiza pakati pawo, palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah ngokhululuka zedi, Ngwachifundo chambiri. info
التفاسير:

external-link copy
183 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُتِبَ عَلَيۡكُمُ ٱلصِّيَامُ كَمَا كُتِبَ عَلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (m’mwezi wa Ramadan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa). info
التفاسير:

external-link copy
184 : 2

أَيَّامٗا مَّعۡدُودَٰتٖۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِيضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٖ فَعِدَّةٞ مِّنۡ أَيَّامٍ أُخَرَۚ وَعَلَى ٱلَّذِينَ يُطِيقُونَهُۥ فِدۡيَةٞ طَعَامُ مِسۡكِينٖۖ فَمَن تَطَوَّعَ خَيۡرٗا فَهُوَ خَيۡرٞ لَّهُۥۚ وَأَن تَصُومُواْ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

(Kusalaku nkwa) masiku owerengeka. Koma amene akhale odwala mwa inu kapena akhale paulendo, (namasula masiku ena), akwaniritse chiwerengerocho m’masiku ena. Ndipo kwa amene sangathe kusala apereke dipo lodyetsa masikini. Ndipo amene achite zabwino mwa chifuniro chake, kutero ndibwino kwa iye. Ndipo kusala (pamene kukulolezedwa kumasula) ndibwino kwa inu, ngati muli odziwadi (kufunika kwa kusala).[19] info

[19] Amene sangathe kusala ndi awa:-
a) Okalamba kwambiri omwe abwerera ku umwana, amene sangathe kupilira
ndi njala
b) Odwala amene sangathe kusala ndipo alibe chiyembekezo choti achira. Anthu oterewa akuloledwa kusiya kusala. Ndipo tsiku lililonse aliyense wa iwo apereke chakudya chokwana kudya munthu mmodzi. Chakudya chomwe anthu m’dzikomo amadya. Koma amene ali osauka asachite zimenezi.
Allah amkhululukira pakuti Allah sakakamiza munthu kuchita chimene sangathe kuchichita.
Tsono wodwala yemwe ali ndi chiyembekezo chochira, ndi wapakati amene akuvutika ndi kusala, ndi woyamwitsa amene akuona kuti azunzika akasala, onsewa sapereka dipo lija. Koma adzalipa masiku amene adamasulawo zikawachokera zovutazo monganso zilili ndi wapaulendo. Koma masheikh ena akuti wapakati ndi woyamwitsa nawonso apereke dipo la chakudya. Tero malangizo awanso tikhoza kuwatsata.
Tsono kunena koti: “Ngati mutasala ndi bwino kwa inu...” kukusonyeza kuti kumanga silamulo lomwe Allah watikakamiza kuchita lopanda phindu kwa ife, koma nchinthu chothandiza kwa anthu, makamaka pathupi lathu.
Ndipo kuonjezera apa, Allah, pa tsiku la chimaliziro, adzatipatsa mphoto yabwino. Masiku ano madokotala onse padziko lapansi akuvomereza kuti kusala kuli ndi phindu lalikulu ku thupi la munthu. Ichi ndi chimodzi mwa zizindikiro zosonyeza kuona kwa chipembedzo cha Chisilamu.
Chinenere nkhaniyi papita zaka zambiri, ndipo tsopano omwe sali Asilamu akuvomereza.

التفاسير:

external-link copy
185 : 2

شَهۡرُ رَمَضَانَ ٱلَّذِيٓ أُنزِلَ فِيهِ ٱلۡقُرۡءَانُ هُدٗى لِّلنَّاسِ وَبَيِّنَٰتٖ مِّنَ ٱلۡهُدَىٰ وَٱلۡفُرۡقَانِۚ فَمَن شَهِدَ مِنكُمُ ٱلشَّهۡرَ فَلۡيَصُمۡهُۖ وَمَن كَانَ مَرِيضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٖ فَعِدَّةٞ مِّنۡ أَيَّامٍ أُخَرَۗ يُرِيدُ ٱللَّهُ بِكُمُ ٱلۡيُسۡرَ وَلَا يُرِيدُ بِكُمُ ٱلۡعُسۡرَ وَلِتُكۡمِلُواْ ٱلۡعِدَّةَ وَلِتُكَبِّرُواْ ٱللَّهَ عَلَىٰ مَا هَدَىٰكُمۡ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza.[20] info

[20] Allah akufuna kuti tikwaniritse chiwerengero cha masiku makumi atatu (30) kapena makumi awiri ndi mphambu zisanu ndi zinayi (29) chifukwa choti phindu lakumanga silingapezeke mthupi la munthu pokhapokha kumangaku kutakwaniritsidwa m’masiku amenewa.

التفاسير:

external-link copy
186 : 2

وَإِذَا سَأَلَكَ عِبَادِي عَنِّي فَإِنِّي قَرِيبٌۖ أُجِيبُ دَعۡوَةَ ٱلدَّاعِ إِذَا دَعَانِۖ فَلۡيَسۡتَجِيبُواْ لِي وَلۡيُؤۡمِنُواْ بِي لَعَلَّهُمۡ يَرۡشُدُونَ

Ndipo akapolo anga akakufunsa za ine, (auze kuti) Ine ndili pafupi nawo. Ndimayankha zopempha za wopempha pamene akundipempha. Choncho iwo ayankhe kuitana kwanga ndipo andikhulupirire kuti aongoke. [21] info

[21] Sikuti iwe wekha ndiwe uzipempha Allah kuti: “Ndipatseni chakuti; nchiritseni kumatenda akutiakuti,” pomwe iwe suvomera kuitana kwa Allah poleka zimene akukuletsa ndi kutsata zimene akukulamula. Yamba kumuvomera Allah usanayambe kumpempha ndiye kuti pempho lako lidzakhala laphindu.

التفاسير: