[6] Apa akutanthauza kuti pamene takutsogolerani ku njira yolunjika, takulolani inu ampingo wa Muhammad (s.a.w) kukhala anthu olungama, kulungama kosapyola nako muyeso ndiponso kopanda kuchepetsa chinthu chilichonse chazauzimu, ndi chamoyo wapadziko lino lapansi. Mpingo wa Asilamu ngwapakatikati mzokhulupilira zake zonse. Umalimbikira kugwira ntchito ya zinthu za mdziko ndiponso ya zinthu zauzimu mwakhama, chilichonse mwa zimenezi amachilimbikira mosapyoza muyeso. Limeneli ndilo tanthauzo la “mpingo wapakatikati.’’ Chisilamu sichilekelera munthu mmodzi kuti apondereze anthu ambirimbiri; ndiponso sichilekelera anthu ambiri kusalabadira za munthu mmodzi.