Vertaling van de betekenissen Edele Qur'an - Chichewa-vertaling - Khalid Ibrahim Beitala

Pagina nummer:close

external-link copy
26 : 76

وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَٱسۡجُدۡ لَهُۥ وَسَبِّحۡهُ لَيۡلٗا طَوِيلًا

Ndipo usiku mlambire Iye, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso umulemekeze usiku nthawi yaitali (popemphera sunna za tahajjudi). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 76

إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ يُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ وَيَذَرُونَ وَرَآءَهُمۡ يَوۡمٗا ثَقِيلٗا

Ndithu awa akukonda moyo wa dziko lapansi, ndipo akulisiya kumbuyo kwao tsiku lovuta. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 76

نَّحۡنُ خَلَقۡنَٰهُمۡ وَشَدَدۡنَآ أَسۡرَهُمۡۖ وَإِذَا شِئۡنَا بَدَّلۡنَآ أَمۡثَٰلَهُمۡ تَبۡدِيلًا

Ife ndi amene tidawalenga ndipo tidalimbika kalengedwe kawo; ndipo titafuna tingabweretse ena onga iwo (omvera Allah) kulowa m’malo mwawo. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 76

إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٞۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا

Ndithu ichi ndichikumbutso choncho amene afuna atsata njira yopitira kwa Mbuye wake (pomukhulupirira ndi kumumvera). info
التفاسير:

external-link copy
30 : 76

وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمٗا

Koma simungafune nokha chilichonse pokhapokha atafuna Allah, ndithu Allah ndi Wodziwa zedi, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 76

يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمِينَ أَعَدَّ لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمَۢا

Akumlowetsa amene wamfuna ku chifundo Chake; koma oyipa wawalinganizira chilango chowawa kwambiri. info
التفاسير: