Vertaling van de betekenissen Edele Qur'an - Chichewa-vertaling - Khalid Ibrahim Beitala

Az-Zumar

external-link copy
1 : 39

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Kuvumbulutsidwa kwa Buku ili kwachokera kwa Allah, Mwini mphamvu zoposa; Mwini nzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 39

إِنَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ فَٱعۡبُدِ ٱللَّهَ مُخۡلِصٗا لَّهُ ٱلدِّينَ

Ndithu Ife takuvumbulutsira iwe buku ili mwamtheradi; choncho mpembedze Allah momyeretsera mapemphero Iye yekha. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 39

أَلَا لِلَّهِ ٱلدِّينُ ٱلۡخَالِصُۚ وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ مَا نَعۡبُدُهُمۡ إِلَّا لِيُقَرِّبُونَآ إِلَى ٱللَّهِ زُلۡفَىٰٓ إِنَّ ٱللَّهَ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡ فِي مَا هُمۡ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ كَٰذِبٞ كَفَّارٞ

Dziwani kuti Allah Ngolandira mapemphero oyera, (opanda kuphatikizidwa ndi zina). Koma amene adzipangira athandizi kusiya Allah, (akumanena kuti): “Ife sitikuwapembedza awa, koma tikutero ndi cholinga choti atifikitse pafupi ndi Allah.” Ndithu Allah, adzaweruza pakati pawo (pakati pa okhulupirira Allah, ndi okana) pa zimene akusiyana. Ndithu Allah saongola amene ali wabodza; wokanira zedi (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 39

لَّوۡ أَرَادَ ٱللَّهُ أَن يَتَّخِذَ وَلَدٗا لَّٱصۡطَفَىٰ مِمَّا يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ

Allah akadafuna kupeza mwana, akadasankha yemwe akum’funa mzomwe adalenga. Wapatukana ndi zimenezo! Iye ndi Allah Mmodzi; Wogonjetsa; (Wochita zimene wafuna). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 39

خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۖ يُكَوِّرُ ٱلَّيۡلَ عَلَى ٱلنَّهَارِ وَيُكَوِّرُ ٱلنَّهَارَ عَلَى ٱلَّيۡلِۖ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِي لِأَجَلٖ مُّسَمًّىۗ أَلَا هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ

Adalenga thambo ndi nthaka mwamtheradi. Amakulunga usiku mu usana; ndipo amakulunga usana mu usiku. Ndipo dzuwa ndi mwezi wazichita kuti zitumikire monga momwe afunira. Zonsezi zikuyenda kufikira pa nthawi yake imene yaikidwa. Dziwani kuti Iye (Allah) Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri. info
التفاسير: