Vertaling van de betekenissen Edele Qur'an - Chichewa-vertaling - Khalid Ibrahim Beitala

Pagina nummer:close

external-link copy
77 : 27

وَإِنَّهُۥ لَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo ndithu iyi (Qur’an) ndichiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
78 : 27

إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُم بِحُكۡمِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo ndi chiweruzo chake (choona); ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa Ngodziwa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
79 : 27

فَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۖ إِنَّكَ عَلَى ٱلۡحَقِّ ٱلۡمُبِينِ

Choncho tsamira kwa Allah; ndithu iwe uli pa njira yachoonadi yoonekera. info
التفاسير:

external-link copy
80 : 27

إِنَّكَ لَا تُسۡمِعُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَلَا تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا وَلَّوۡاْ مُدۡبِرِينَ

Ndithu iwe sungathe kuwachititsa kuti amve kuitana kwako akufa, ndiponso sungathe kuwachititsa kuti agonthi amve kuitanako, pamene akucheuka kutembenuza misana (osafuna kumva ulaliki wako). info
التفاسير:

external-link copy
81 : 27

وَمَآ أَنتَ بِهَٰدِي ٱلۡعُمۡيِ عَن ضَلَٰلَتِهِمۡۖ إِن تُسۡمِعُ إِلَّا مَن يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُم مُّسۡلِمُونَ

Ndiponso suli owaongola akhungu m’kusokera kwawo, ndipo sungachititse kuti amve (uthenga wako) kupatula yemwe akukhulupirira Ayah (ndime) Zathu; iwowo ndiwo Asilamu (ogonjera malamulo Athu). info
التفاسير:

external-link copy
82 : 27

۞ وَإِذَا وَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِمۡ أَخۡرَجۡنَا لَهُمۡ دَآبَّةٗ مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ تُكَلِّمُهُمۡ أَنَّ ٱلنَّاسَ كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا لَا يُوقِنُونَ

Ndipo mawu (onena kudza kwa Qiyâma) akadzatsimikizika pa iwo, tidzawatulutsira chinyama m’nthaka chimene chidzawayankhula kuti ndithu anthu adalibe chitsimikizo pa Ayah (ndime) Zathu. info
التفاسير:

external-link copy
83 : 27

وَيَوۡمَ نَحۡشُرُ مِن كُلِّ أُمَّةٖ فَوۡجٗا مِّمَّن يُكَذِّبُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُمۡ يُوزَعُونَ

Ndipo (akumbutse za) tsiku lormwe tidzasonkhanitsa magulumagulu mu m’badwo uliwonse omwe amatsutsa Ayah (ndime) Zathu. Ndipo iwo adzakhala magulumagulu. info
التفاسير:

external-link copy
84 : 27

حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُو قَالَ أَكَذَّبۡتُم بِـَٔايَٰتِي وَلَمۡ تُحِيطُواْ بِهَا عِلۡمًا أَمَّاذَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Kufikira pomwe adzaza; (Allah) adzati: “Kodi inu mudazitsutsa Ayah (ndime) Zanga popanda kuzidziwa bwinobwino, nanga mumachita chiyani?” info
التفاسير:

external-link copy
85 : 27

وَوَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِم بِمَا ظَلَمُواْ فَهُمۡ لَا يَنطِقُونَ

Ndipo mawu onena za kuonongeka adzatsimikizika pa iwo, chifukwa cha chinyengo chawo (chodzichitira okha) ndipo iwo sadzawiringula. info
التفاسير:

external-link copy
86 : 27

أَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا جَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِيَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ

Kodi saona kuti Ife tapanga usiku ndi cholinga chakuti apumule m’menemo, ndinso usana woyera (kuti aone)? Ndithu mu zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
87 : 27

وَيَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَفَزِعَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا مَن شَآءَ ٱللَّهُۚ وَكُلٌّ أَتَوۡهُ دَٰخِرِينَ

Ndipo (akumbutse za) tsiku limene lipenga (la chiweruziro) lidzaimbidwa, adzadzidzimuka amene ali kumwamba ndi amene ali pansi kupatula yemwe Allah wamfuna (kuti adzadzidzimuke); ndipo onse adzamdzera (Allah) ali odzichepetsa (ofooka). info
التفاسير:

external-link copy
88 : 27

وَتَرَى ٱلۡجِبَالَ تَحۡسَبُهَا جَامِدَةٗ وَهِيَ تَمُرُّ مَرَّ ٱلسَّحَابِۚ صُنۡعَ ٱللَّهِ ٱلَّذِيٓ أَتۡقَنَ كُلَّ شَيۡءٍۚ إِنَّهُۥ خَبِيرُۢ بِمَا تَفۡعَلُونَ

Ndipo udzawaona mapiri ndi kuwaganizira kuti akhazikika pomwe akuyenda kuyenda kwa mitambo. Chimenecho ndichikonzero cha Allah chimene adakonzera chinthu chilichonse. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene muchita. info
التفاسير: