[372] Nkhani yaikulu imene akafiri (anthu osakhulupilira Allah) adali kufunsana wina ndi mnzake ndi nkhani yakuuka tsiku la Qiyâma ndi uneneri wa Mtumiki Muhammad. Amafunsana kuti, “Kodi nzoona tidzauka m’manda, nanga nzoona kuti Muhammad ndi Mneneri?” Adali kufunsananso kuti, “Kodi zakuti Allah ndi Mmodzi ndi zoona?”
[374] Allah, apa, akuwauza kuti asiye kuganizira zinthu zopanda pake. Kodi sadadziwebe mpaka pano kuti Muhammad ndi Mneneri wa Allah, ndikuti Allah ndi Mmodzi yekha? Ndikutinso kuli tsiku lachimaliziro; pamene munthu aliyense adzalipidwa pa zimene adachita? Basi tsiku lachimaliziro likadzawafikira adzadziwa kuti zimene adali kuwauza Mneneri nzoona.
[375] Kuyambira Ayah iyi, kudzafika Ayah 16, Allah akusonyeza anthu Ake madalitso ambiri omwe wawadalitsa nawo kuti azindikire kuti Mwini kupereka madalitso amenewa m’dziko sangawasiye anthu Ake m’kusokera popanda kuwatumizira munthu wowaongolera ku njira yabwino, ndikuwadziwitsa zamtendere wapadziko ndi tsiku lachimaliziro. Ndikuti Allah amene adapanga zonsezi palibe chimene angachilephere. Ndipo tanthauzo la choyala, apa, ndi pamalo poti nkutheka munthu kuchita chimene akufuna pa moyo wake. Tanthauzo lake sikuti dothi lakhala ngati mkeka wa pabedi ayi.
[376] Apa, ndikuti zimene munthu amaziona patsogolo pake nkumaziganizira ngati madzi pomwe sali madzi. Choncho pa tsiku limenelo mapiri adzaoneka ngati akhazikika monga m’mene adalili pomwe sichoncho, adzakhala ngati thonje louluka ndi mphepo.
[377] Jahannam ndi dzina lamoto wodziwika wa tsiku lachimaliziro. Apa Allah akutidziwitsa kuti Jahannam ndi malo amene akudikira akafiri kuti m’menemo akalipidwe malipiro awo chifukwa chokanira aneneri pambuyo powasonyeza zizindikiro zoti iwo ndi aneneri a Allah. Ndiponso kumulakwira Allah pochita zimene adaletsa monga; kukana umodzi wa Allah, kukana utumiki wa Mahammad (s.a.w) ndi kukana uthenga wa Qur’an. Komanso kugwa mmachimo osiyanasiyana.
[378] Chipembedzo cha Chisilamu chikuphunzitsa kuti pali zisangalalo ziwiri: Chisangalalo cha mzimu ndi chisangalalo cha thupi. Tsono chisangalalo cha mzimu ndiko kuyanjana kochokera kwa Allah kumene anthu Ake abwino adzakupeza. Chisangalalo cha thupi ndi monga m’mene afotokozera mu Ayah iyi ndi msura zina. Zokondweretsa monga minda, akazi okongola, mowa (osaledzeretsa) ndiponso sikudzakhala kumva chilichonse chokhumudwitsa.
Taonani, zoledzeretsa ndi zoletsedwa padziko lino lapansi chifukwa cha zoipa zake. Koma mowa wa patsiku la Qiyâma udzakhala wopanda zoipa.