ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

An-Naba’

external-link copy
1 : 78

عَمَّ يَتَسَآءَلُونَ

۞ Kodi akufunsana zachiyani? info
التفاسير:

external-link copy
2 : 78

عَنِ ٱلنَّبَإِ ٱلۡعَظِيمِ

Za nkhani yayikulu ija. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 78

ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ مُخۡتَلِفُونَ

Imene iwo akusiyana (maganizo).[372] info

[372] Nkhani yaikulu imene akafiri (anthu osakhulupilira Allah) adali kufunsana wina ndi mnzake ndi nkhani yakuuka tsiku la Qiyâma ndi uneneri wa Mtumiki Muhammad. Amafunsana kuti, “Kodi nzoona tidzauka m’manda, nanga nzoona kuti Muhammad ndi Mneneri?” Adali kufunsananso kuti, “Kodi zakuti Allah ndi Mmodzi ndi zoona?”

التفاسير:

external-link copy
4 : 78

كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ

Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa.[373] info

[373] Kuyankhula koti: “Kallaa” kwanenedwa kwambiri m’Qur’an. Tanthauzo lake nthawi zina ndikuletsa, nthawi zina ndikutsimikiza. Choncho mawuwa amatanthauzidwa malinga ndi momwe chiganizocho chilili.

التفاسير:

external-link copy
5 : 78

ثُمَّ كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ

Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira).[374] info

[374] Allah, apa, akuwauza kuti asiye kuganizira zinthu zopanda pake. Kodi sadadziwebe mpaka pano kuti Muhammad ndi Mneneri wa Allah, ndikuti Allah ndi Mmodzi yekha? Ndikutinso kuli tsiku lachimaliziro; pamene munthu aliyense adzalipidwa pa zimene adachita? Basi tsiku lachimaliziro likadzawafikira adzadziwa kuti zimene adali kuwauza Mneneri nzoona.

التفاسير:

external-link copy
6 : 78

أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ مِهَٰدٗا

Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala?[375] info

[375] Kuyambira Ayah iyi, kudzafika Ayah 16, Allah akusonyeza anthu Ake madalitso ambiri omwe wawadalitsa nawo kuti azindikire kuti Mwini kupereka madalitso amenewa m’dziko sangawasiye anthu Ake m’kusokera popanda kuwatumizira munthu wowaongolera ku njira yabwino, ndikuwadziwitsa zamtendere wapadziko ndi tsiku lachimaliziro. Ndikuti Allah amene adapanga zonsezi palibe chimene angachilephere. Ndipo tanthauzo la choyala, apa, ndi pamalo poti nkutheka munthu kuchita chimene akufuna pa moyo wake. Tanthauzo lake sikuti dothi lakhala ngati mkeka wa pabedi ayi.

التفاسير:

external-link copy
7 : 78

وَٱلۡجِبَالَ أَوۡتَادٗا

Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)? info
التفاسير:

external-link copy
8 : 78

وَخَلَقۡنَٰكُمۡ أَزۡوَٰجٗا

Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 78

وَجَعَلۡنَا نَوۡمَكُمۡ سُبَاتٗا

Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 78

وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِبَاسٗا

Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 78

وَجَعَلۡنَا ٱلنَّهَارَ مَعَاشٗا

Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo; info
التفاسير:

external-link copy
12 : 78

وَبَنَيۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعٗا شِدَادٗا

Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba; info
التفاسير:

external-link copy
13 : 78

وَجَعَلۡنَا سِرَاجٗا وَهَّاجٗا

Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa); info
التفاسير:

external-link copy
14 : 78

وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءٗ ثَجَّاجٗا

Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula; info
التفاسير:

external-link copy
15 : 78

لِّنُخۡرِجَ بِهِۦ حَبّٗا وَنَبَاتٗا

Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 78

وَجَنَّٰتٍ أَلۡفَافًا

Ndi minda yothothana nthambi za mitengo. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 78

إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ كَانَ مِيقَٰتٗا

Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 78

يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجٗا

Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 78

وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبٗا

Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 78

وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا

Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu.[376] info

[376] Apa, ndikuti zimene munthu amaziona patsogolo pake nkumaziganizira ngati madzi pomwe sali madzi. Choncho pa tsiku limenelo mapiri adzaoneka ngati akhazikika monga m’mene adalili pomwe sichoncho, adzakhala ngati thonje louluka ndi mphepo.

التفاسير:

external-link copy
21 : 78

إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتۡ مِرۡصَادٗا

Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 78

لِّلطَّٰغِينَ مَـَٔابٗا

Mbuto ya opyola malire.[377] info

[377] Jahannam ndi dzina lamoto wodziwika wa tsiku lachimaliziro. Apa Allah akutidziwitsa kuti Jahannam ndi malo amene akudikira akafiri kuti m’menemo akalipidwe malipiro awo chifukwa chokanira aneneri pambuyo powasonyeza zizindikiro zoti iwo ndi aneneri a Allah. Ndiponso kumulakwira Allah pochita zimene adaletsa monga; kukana umodzi wa Allah, kukana utumiki wa Mahammad (s.a.w) ndi kukana uthenga wa Qur’an. Komanso kugwa mmachimo osiyanasiyana.

التفاسير:

external-link copy
23 : 78

لَّٰبِثِينَ فِيهَآ أَحۡقَابٗا

Adzakhala m’menemo muyaya. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 78

لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدٗا وَلَا شَرَابًا

Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo); info
التفاسير:

external-link copy
25 : 78

إِلَّا حَمِيمٗا وَغَسَّاقٗا

Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto); info
التفاسير:

external-link copy
26 : 78

جَزَآءٗ وِفَاقًا

Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 78

إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابٗا

Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah); info
التفاسير:

external-link copy
28 : 78

وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كِذَّابٗا

Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 78

وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ كِتَٰبٗا

Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 78

فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا

Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 78

إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ مَفَازًا

Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 78

حَدَآئِقَ وَأَعۡنَٰبٗا

Minda ndi zipatso za mphesa. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 78

وَكَوَاعِبَ أَتۡرَابٗا

Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 78

وَكَأۡسٗا دِهَاقٗا

Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 78

لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوٗا وَلَا كِذَّٰبٗا

Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 78

جَزَآءٗ مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابٗا

Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira.[378] info

[378] Chipembedzo cha Chisilamu chikuphunzitsa kuti pali zisangalalo ziwiri: Chisangalalo cha mzimu ndi chisangalalo cha thupi. Tsono chisangalalo cha mzimu ndiko kuyanjana kochokera kwa Allah kumene anthu Ake abwino adzakupeza. Chisangalalo cha thupi ndi monga m’mene afotokozera mu Ayah iyi ndi msura zina. Zokondweretsa monga minda, akazi okongola, mowa (osaledzeretsa) ndiponso sikudzakhala kumva chilichonse chokhumudwitsa.
Taonani, zoledzeretsa ndi zoletsedwa padziko lino lapansi chifukwa cha zoipa zake. Koma mowa wa patsiku la Qiyâma udzakhala wopanda zoipa.

التفاسير:

external-link copy
37 : 78

رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابٗا

Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero); info
التفاسير:

external-link copy
38 : 78

يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ صَفّٗاۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابٗا

Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 78

ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا

Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi). info
التفاسير:

external-link copy
40 : 78

إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابٗا قَرِيبٗا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا

Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi). info
التفاسير: