Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
197 : 2

ٱلۡحَجُّ أَشۡهُرٞ مَّعۡلُومَٰتٞۚ فَمَن فَرَضَ فِيهِنَّ ٱلۡحَجَّ فَلَا رَفَثَ وَلَا فُسُوقَ وَلَا جِدَالَ فِي ٱلۡحَجِّۗ وَمَا تَفۡعَلُواْ مِنۡ خَيۡرٖ يَعۡلَمۡهُ ٱللَّهُۗ وَتَزَوَّدُواْ فَإِنَّ خَيۡرَ ٱلزَّادِ ٱلتَّقۡوَىٰۖ وَٱتَّقُونِ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ

(Mapemphero a) Hajj ali ndi miyezi yodziwika, (yomwe ndi: Shawwal, Dhul Qa’da ndi Dhul Hijjah). Amene watsimikiza kuchita Hajj m’miyezi imeneyo, asachite ndi kuyankhula zauve, ndiponso asapandukire malamulo (pochita zoletsedwa uku iye ali m’mapemphero a Hajj), ndiponso asakangane ali m’Hajjimo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, Allah achidziwa. Ndipo dzikonzereni kamba wa paulendo, ndithu kamba wabwino (wadziko lapansi) ndi amene angakupewetseni kupemphapempha, (koma kamba wabwino wa tsiku lachimaliziro ndiko kuopa Allah). Choncho ndiopeni inu eni nzeru. info
التفاسير:

external-link copy
198 : 2

لَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَبۡتَغُواْ فَضۡلٗا مِّن رَّبِّكُمۡۚ فَإِذَآ أَفَضۡتُم مِّنۡ عَرَفَٰتٖ فَٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ عِندَ ٱلۡمَشۡعَرِ ٱلۡحَرَامِۖ وَٱذۡكُرُوهُ كَمَا هَدَىٰكُمۡ وَإِن كُنتُم مِّن قَبۡلِهِۦ لَمِنَ ٱلضَّآلِّينَ

Sikulakwa kwa inu kufunafuna zabwino kwa Mbuye wanu (pogulitsa zinthu zanu uku muli m’mapemphero a Hajj, kapena kugula). Ndipo mukabwerera kuchokera ku Arafat, tamandani Allah pamalo otchedwa Masha’r Harâm (Muzdalifa). Ndipo mkumbukireni monga momwe adakutsogolerani, chikhalirecho kale mudali mwa osokera. info
التفاسير:

external-link copy
199 : 2

ثُمَّ أَفِيضُواْ مِنۡ حَيۡثُ أَفَاضَ ٱلنَّاسُ وَٱسۡتَغۡفِرُواْ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Kenako yendani limodzi kuchokera pamalo pamene akuchokerapo anthu onse (pomwe ndi pa Arafat), ndipo pemphani chikhululuko kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
200 : 2

فَإِذَا قَضَيۡتُم مَّنَٰسِكَكُمۡ فَٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ كَذِكۡرِكُمۡ ءَابَآءَكُمۡ أَوۡ أَشَدَّ ذِكۡرٗاۗ فَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَقُولُ رَبَّنَآ ءَاتِنَا فِي ٱلدُّنۡيَا وَمَا لَهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ مِنۡ خَلَٰقٖ

Ndipo mukamaliza mapemphero anu (tsiku la Idi komwe ndikuponya sangalawe, kuzinga nyama za nsembe, kumeta ndi kuzungulira Ka’aba (Tawaful Ifâda), mtamandeni Allah monga momwe mudali kutamandira makolo anu kapena mtamandeni koposa. Ndipo alipo ena mwa anthu amene akunena (kuti): “E Mbuye wathu! Tipatseni padziko lapansi.” Ndipo iwo alibe gawo lililonse pa tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
201 : 2

وَمِنۡهُم مَّن يَقُولُ رَبَّنَآ ءَاتِنَا فِي ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٗ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ حَسَنَةٗ وَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ

Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
202 : 2

أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ نَصِيبٞ مِّمَّا كَسَبُواْۚ وَٱللَّهُ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ

Iwo ali ndi gawo la zimene adachita; ndipo Allah Ngwachangu pakuwerengera. info
التفاسير: